Photo Credit : Gianluigi Guercia
Pofika mwezi uno, dziko la Malawi lapeza ndalama zokwana $2 million (pafupifupi K3.4 billion) kuchoka ku ndondomeko yotumiza achinyamata kukagwira ntchito mu dziko la Israel.
Izi ndi malingana ndi nduna yowona zachuma, a Simplex Chithyola Banda.
A Chithyola Banda ati pakutha pa mwezi uno, akuyembekezera kuti dziko lino likhala litapeza $1 million (pafupifupi K1.7 billion) yowonjezera.
Iwo ati izi zikuthandiza dziko lino kumbali yopeza ndalama zakunja mosavuta.