Malawi Broadcasting Corporation
Crime Local Local News Nkhani

Malaulo: Anjatidwa atagwililira mwana omupeza pofuna kukhwima

Khoti lina m’boma la Phalombe lalamula a Paul Mwina a zaka 35 zakubadwa kuti akagwire jele kwa zaka 14 chifukwa adagwililira mwana omupeza wazaka 12 pofuna kulemera.

Ofalitsankhani pa Polisi ya m’bomali, a Jimmy Kapanja, ati bamboyu adapita kwa sing’anga wina pofuna kukhwima kuti alemere ndipo atabwera ndilufotokozera mkazi wake zoyenera kuchita, sadazengereze koma kulolera malodzawo.

Komabe mwanayo adakatsina khutu m’bale wake, yemwe adakatula nkhaniyi ku Polisi.

A Mwina ndi a m’mudzi mwa Volupo, mfumu yayikulu Nkhulambe m’boma la Phalombe lomwelo.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Maranatha yatumiza ana ambiri ku sukulu za ukachenjede

Simeon Boyce

President Dr Chakwera meets religious leaders

MBC Online

CFTC to probe sugar price hike

Earlene Chimoyo
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.