Gulu la mabungwe omwe si aboma m’dziko muno la Citizen Alliance layamikira boma pa zomwe likuchita pobwezera m’chimake chuma cha dziko lino.
Muchikalata chomwe achiwerenga pa msonkhano wa atolankhani ku Lilongwe, akuluakulu a bungweli ati mwazina, boma lakwanitsa kupezanso chikhulupiliro pachuma ku maiko akunja, zomwe zachititsa kuti ayambenso kuthandiza dziko lino.
Iwo ati kubwera kwa ndalama zokwana $175 million kuchokera Ku IMF komanso $80 million kuchokera ku World Bank ndichitsimikizo cha ntchito yabwino yomwe boma lagwira.
Wapampando wa mabungwewa, a Masauko Thawe, ati ndizosangalatsa kuti ndalama zakunja zikupezeka m’dziko muno ndipo ayamikira boma pa chitukuko cha zomangamanaga monga misewu, sukulu ndi zipatala, zimene ati zithandiza kukweza dziko lino.
Komabe wo ati m’dziko muno mukadali mavuto monga katangale, kuchuluka kwa ngongole, mavuto pa kayendetsedwe ka chuma, katoleredwe ka misonkho, mwazina, zimene boma likuyenera kukonza.