Akatswiri azachuma komanso ufulu wachibadwidwe ayamikira boma chifukwa ka ndondomeko zoyenera zokonzeranso chuma cha dziko lino zomwe akuti zapangitsa a World Bank kupereka thandizo la $80 million (pafupifupi K140 billion) yokwezera chuma cha dziko lino.
Wapampando wa mgwirizano wa mabungwe 250 lotchedwa National Advocacy Platform, a Benedicto Kondowe, ati ndalamazi zithandiza kukweza umoyo wa aMalawi munjira zosiyanasiyana.
Nawo a Undule Mwakasungula ati nkhaniyi ndiyokomera mMalawi aliyense wakufuna kwabwino, makamaka pozindikira kuti mabungwe akunja akhala asakuthandiza dziko lino kwa zaka khumi kaamba kakusokonekera kwa kayendetsedwe ka chuma.
Katswiri wa zachuma, Emmanuel Soko, wati Malawi akufuna thandizo laulere osati ngongole pa ntchito yomanganso chuma chake.
Sabata yatha, African Development Bank nayo inathandiza bajeti ya Malawi ndi $23 million.
Olemba: Blessings Cheleuka