Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Sports Sports

Mabedi waitananso Gaba

Dan Chemis, amene ndi m’modzi mwa amene amayankhulapo paza masewero ampira wamiyendo, wati zimene mphunzitsi wa timu ya The Flames, Patrick Mabedi, wachita poyitananso Frank Gabadinho Mhango zikusonyeza kuti mphunzitsiyu ndi oleza mtima komanso kudziwa bwino ntchito yake.

Poyankhulapo, a Chemis ati a Mabedi sanaonetse chidani potengera kusamvana komwe kunalipo posachedwapa pakati pa awiriwa.

“Izi ndi za dziko ndipo mukaona anzathu aku Zambia, aitanitsa akatswiri awo onse, ifenso tinayenera kutero chifukwa zitithandiza kukonzekera ndithu. Osewera amene alipowa akufunika kuti aphunzire zambiri kwa Gaba popeza iye akukula,” iwo anatero.

M’mbuyomu, a Mabedi akhala asakumutenga Gaba pazokonzekera masewero ena alionse a Flames kaamba koti anaachedwa kuti akakumane ndi osewera amnzake nthawi imene timuyi imachita zokonzekera kuti ikakumane ndi timu ya Liberia m’mwezi wa November chaka chatha.

Malawi ikuyembekezeka kuchititsa mpikisano wa mayiko anayi omwe matimu a Zambia, Kenya ndi Zimbabwe adzatengepo mbali ngati mbali imodzi yokonzekera mpikisano wa World Cup, omwe udzachitike m’chaka cha 2026.

Mphunzitsiyu lero watulutsa m’ndandanda wa osewera okwana 32 ndipo ena mwa iwo ndi amene amasewera kunja kwa maiko a Africa.

M’buyomu a Mabedi anaitanitsa osewera 27 amene amasewera m’dziko muno kuti akatenge nawo gawo pa mpikisanowu omwe ukhale ukuchitikira mu mzinda wa Lilongwe pa bwalo la masewero la Bingu kuyambira pa 18 mpakana pa 26 March chaka chino.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Police sweep results in arrest of 22 individuals

Romeo Umali

Nzika yaku Mozambique ayigwira itathyola ndikuba mnyumba

Charles Pensulo

President Chakwera returns to Lilongwe

Kumbukani Phiri
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.