Ma Banki asanu ndi atatu a m’dziko muno apanga phindu lokwana K256.7 billion m’chaka cha 2023 chokha, boma litadulapo kale msonkho.
Izi ndi malingana ndi lipoti la m’mene chuma chikuyendera m’dziko muno lochokera ku banki yayikulu pa dziko lonse (World Bank).
Lipotili lati phinduli lakwera kuchoka pa K170.8 billion lowe ma banki-wa anapeza m’chaka cha 2022.
Bankiyi yati ngakhale chuma cha dziko lino chakumana ndi mavuto ambiri, gawo la mabanki likupitilira kukwera komanso kupeza phindu lochuluka.