Boma, kudzera ku unduna oona za ulimi m’dziko muno, lachenjeza alimi komanso a Malawi kuti kuzembetsa fodya ndi kukamugulitsa m’maiko ena ndi kusakonda dziko lino.
A Geoffrey Mamba, amene ndi mlembi ku undunawu, ndi wapereka chenjezoli pamene amatsegulira msika wa fodya mu mzinda wa Mzuzu.
Iwo ananenetsa kuti lamulo lidzagwira ntchito kwa onse amene adzawapeze akuchita m’chitidwe wa chinyengowu.
“Fodya ndi mbewu yotetezedwa ndipo sitingalore kuti anthu ena atibere phindu lathu,” a Mamba anafotokoza.
Alimi amene MBC Digital yayankhula nawo ku Mzuzuko aonetsa kukondwa kaamba ka mitengo yomwe ogula akupereka, popeza mitengo yomwe ogula akupereka pa fodya wa contract ndi $3.15 komanso $2.99.
Olemba: George Mkandawire