Mlangizi wa zamaphunziro ku Zone ya Kabuthu ku Lilongwe, a Efrida Ndau, walimbikitsa aphunzitsi a msukulu za primary m’dziko muno kuphunzitsa ophunzira awo m’magulu.
Malinga ndi a Ndau, kuphunzitsa mwamtunduwu kumathandiza kuti ophunzira adzikhala ndi chidwi pamaphunziro komanso kugawana nzeru mosavuta.
A Ndau anena izi pomwe mtsogoleri wa bungwe la Japanese International Corporation Agency (JICA), a AkihikoTanaka, anayendera zina mwantchito za maphunziro zomwe zili pansi pabungweli mderali.
A Tanaka ayamikira ubale omwe ulipo pakati pa aphunzitsi am’dziko muno, ophunzira komanso aphunzitsi omwe anachoka ku dziko la Japan kudzagwira ntchito yophunzitsa msukulu za primary m’dziko muno modzipereka.