Wapampando wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP) m’chigawo chapakati, a Patrick Zebron Chilondola, wati ufulu wopikisana pa maudindo wosiyanasiyana kumene kulipo ndi chitsimikizo kuti chipanichi chimalemekeza ufulu wa demokalase.
Poyankhula ndi MBC pa Madisi Trading Centre pomwe mtsogoleli wadziko lino Dr Lazarus Chakwera anaima kupeleka moni kwa khwimbi lomwe linasonkhana pa malowa lolemba, a Chilondola anati MCP ndi chipani cha dziko lonse.
Pamasamba a mchezo pakhala pakuyenda zithunzi za anthu osiyanasiyana amene anthu akuwaikapo ngati oyenelera kudzatsogolela pa maudindo osiyanasiyana ku chipani cha MCP.
Mlembi wamkulu wa chipani cha MCP, a Eisenhower Mkaka, anati zikusonyezeratu kuti akuluakulu achipanichi ndi mamembala onse akugwirizana kwathunthu kuti Dr Chakwera, yemwenso ndi Prezidenti wa chipani cha MCP, ndiye adzaimire chipanichi pa chisankho cha 2025.
Chipani cha MCP chikuyembekeza kuchititsa msonkhano wake waukulu (convention) m’mwezi wa August chaka chino.
Anthu amene adzasankhidwe akuyembekezeka kudzatsogolera chipanichi kwa zaka zisanu.