Malawi Broadcasting Corporation
Business Development Local Local News Nkhani

KAMPANI ZACHITA BWINO CHAKA CHATHA— MCCCI

Kafukufuku yemwe bungwe la amalonda la Malawi Confederation of Chambers of Commerce and Industry (MCCCI) lachita waonetsa kuti kampani 50 mwa 100 zilizonse m’dziko muno zinapanga ndikugulitsa katundu ochulukirapo chaka chatha ndipo kampani 76 mwa 100 zilizonse ziwonjezera katundu wina chaka chino.

Kafukukufuyu wawonetsanso kuti kampani 32 mwa 100 zilizonse zawonjezera ogwira ntchito chaka chatha ndipo chaka chino, kampani 58 mwa 100 zilizonse ziwonjezera ogwira ntchito.

MCCCI yapezanso kuti chaka chatha, kampani 51 mwa 100 zilizonse zawonjezera ndalama zokwezera malonda (investment) ndipo chaka chino kampani 77 mwa 100 zilizonse ziwonjezera ndalamazi.

Bungweli lati magawo owonjezera kupanga katundu, kulemba anthu ntchito, komanso kuwonjezera ndalama zopititsa patsogolo malonda achita bwino poyelekeza ndi chaka cha 2022.

Ilo lati izi ndi kaamba kakuti zinthu zambiri monga magetsi zinayenda bwino chaka chatha.

Bungweli likuyembekezera kuti chaka chino, zinthu zikhala bwino kwambiri kumbali yamalonda pamene chuma chikwera ndi 3.2 percent kuchoka pa 1.5 percent chaka chatha.

Olemba: Justin Mkweu

#MBCOnlineServices

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Immigration officers picked for questioning

Lonjezo Msodoka

Self-help initiatives springing up in Mwanza

MBC Online

Another BT derby awaits in FDH Bank Cup

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.