Ofalitsankhani za Tobacco Commission, a Telephorus Chigwenembe, wati pali kampani khumi ndi zimene zikhale zikugula fodya chaka chino, kuphatikizapo ya Nyasa Manufacturing Company.
Iwo atinso fodya wolemela makilogalamu 140 million ndiye akuyembekezeka kumugulitsa pa msika wa fodya.
Dziko la Malawi lili ndi misika ya fodya inayi ya kampani ya Auction Holdings Limited ndipo ili ku Mzuzu, Limbe, Kanengo komanso Chinkhoma.
Mtsogoleri wadziko lino, Dr Lazarus Chakwera, ndiye akatsekulire msika wa chaka chino mawa ku Kasungu.
Ndipo m’modzi mwa alimi afodya kwa Chakhaza m’boma la Dowa, a Lyson Artwell Banda, ayamika bungwe la National Economic Empowerment Fund kaamba koonetsetsa kuti alimi akupindula ndi ngongole zomwe akhala akupeleka kwa alimi.
Iwo ati atengako ngongole katatu konse ndipo yoyamba idali K3 million ndipo adayibweza m’miyezi isanu ndi umodzi.
Iwo ati panopa adatenga ngongole ya ndalama zokwana K60 Million, ndipo akuyembekezeka kudinda ma belo a fodya oposa 1,500 ndipo akukwanitsa kulipira antchito oposa 500.
“Ndiyamike boma la Dr Chakwera chifukwa choonetsetsa kuti alimi akupindula mu njira zosiyanasiyana zomwe zikuthandizira pa masomphenya a dziko la Malawi a MW2063,” anatelo a Banda.
A Banda ati ali ndi chiyembekezo kuti kampani zogula fodya ziwagula pa mitengo yabwino kaamba kakuti pakhala mpikisano.