Gulu lovina dansi pa pologalamu yapa wailesi ya Kale Langa imene imauluka pa MBC Radio one yasonkhana mu mzinda wa Mzuzu kumene akuvina dansiyo.
Mkonzi komanso muulutsi wa Pologalamuyo Sol Rasheed wati ndi okondwa kuti wachititsa Pologalamuyo live mu Mzinda wa Mzuzu kumenenso akuti wakumana ndi anthu amene amangowamva akamalemba kalata zawo pa Wailesi.
Anthuwo asangalala ndi Nyimbo za Simanjemanje komanso Kanindo zimene awonetsa luso lawo mmene amkachitira kalero popalasa fumbi mu dansi yobetcha imene amkavina mu nthawi yawo.
Wolemba: Hassan Phiri