Katswiri pankhani yochita zisudzo zapakanema mdziko la Nigeria, John Ikechukwu Okafor, yemwe amatchuka ndi dzina loti Mr Ibu, wamwalira munzinda wa Lagos.
Malinga ndi nyumba zoulutsa mawu m’dzikolo, malipoti akuchipatala akusonyeza kuti nthenda ya mtima kapena kuti Cardiac Arrest ndiyo yatengera katakweyu kulichete loweruka.
Malipotiwa akusonyezanso kuti Mr Ibu wakhala akuvutika ndi ndinthenda yakutseka kapena kuuma kwamagazi m’misempha kufikira pomwe chaka chatha akubanja analengeza kuti mwendo wakatswiriyu wadulidwa ngati mbali imodzi yopulumutsa moyo.
Malinga ndi mkulu wa bungwe loona za anthu ochita zisudzo m’dziko la Nigeria la Actors Guild of Nigeria, a Emeka Rollas Ejezie, Mr Ibu asiya mkazi ndi ana atatu.
Mr Ibu amwalira ali ndi zaka 62 ndipo anaoneka mumafilimu oposa 200 m’dziko la Nigeria.