20/04/17

Written by  Newsroom

Amugulura mano anai kamba ka mkazi
Mnyamata wina pa sitolo zapa Kamchere m’boma la Mchinji amugulula mano anai polimbirana mkazi.

20
April

Watitumizira nkhaniyi wati mtsikana wina m’deralo anapalana ubwenzi ndi anyamata awiri omwe samadziwana. Ubwenzi wa mtsikana ndi anyamatawo unayaka moto ndipo mmodzi mwa anyamatawo kuwalira anzake ponena kuti iye amadziwa kusankha kotero kuti ali pa ubwenzi ndi mtsikana wakuti-wakuti. Nkhaniyi inakampeza mnyamata winayo koma amasowa kuti amufunsa bwanji m’nzakeyo kamba koti samakhulupilira nkhaniyi chifukwa mtsikanayo ali ndi khalidwe lopusitsa. Koma tsiku lina anyamatawo anakakomana ku nyumba kwa mtsikanayo ndipo aliyense anali wodabwa kuona m’nzake. Mmodzi mwa anyamatawo anafunsa mzake yemwe amachita matamayo paza mtsikanayo ndipo awiriwo sanamvane kotero kuti anayamba kuponyerana zibakera. Ndipo m’modzi mwa anyamatawo amaponya zibakera zomwe zimafikira winayo monga matalala mpaka kumuchotsa m’nzakeyo mano anai. Pakadali pano anthu mderalo akuwaseka anyamatawo kamba kokunthana polimbirana mkazi yemwe onsewo samukwatira.

 

Mtsikana wina ayenda zamadulira ku Lilongwe

Mtsikana wina wa zaka pafupifupi twenty ku Phili la Njuzi m’boma la Lilongwe akuyenda zamadulira. Yemwe watumiza nkhaniyi wati mderalo muli mtsikana wina yemwe wateketsa mitima ya amuna ambiri malinga ndi mavalidwe komanso kuti akafunsira amuna. Mtsikanayo yemwe ndi wophunzira pa sukulu ina amavala zovala zazifupi komanso zothina kwambiri. Makolo komanso aphunzitsi ake omwe alephere kumulangiza poti mtsikanayo amati ndu ufulu wake kutero kuthinitsako. Ndipo iye akapeza mwamuna yemwe ndiwopeza saumila mau ndipo amaumilira mwamunayo mpaka atavomela. Ndipo masiku apitawo mtsikanayo anafunsira mphunzitsi wapa sukulu ina yemwenso ndi okwatira ndipo ali ndi ana akulu akulu ofanana msinkhu ndi mtsikanayo. Apo mphunzitsiyo anangoti laponda la mphawi. Koma ubwenziwo utafumbira mpheketsera inamufika ku banja la phunzitisiyo. Kubeba kwa ubwenzi wa anthu awiriwo kunachittsa kuti mkuluyo ayambe kulephere kutumikira banja lake monga momwe amachitira kale. Izi zinachititsa kuti banja la mkuluyo liyambe kuvutika kwambiri. Koma ana amphunzitsiyo atatopa ndi nkhani anangoti pasavute iwo athana ndi mtsikanayo. Ndipo dzana dzanali anawo pamodzi ndi mai awo adakatuwitsa mtsikana ndizibakera pofuna kumuphunzitsa kuipa kochita chibwenzi ndi tate awo. Anthu mderalo ayamika anawo kamba kophunzintsa mtsikanayo mwambo popeza aka sikoyamba kuti mtsikanayo asokoneza banja mderalo. M’mbuyomu mtsikanayo adatsokonezanso banja la mkulu wina wa zamalonda mderalo. Pakadali pano mtsikakanayo sakutuluka mnyumba kamba kamantha poti mkazi wamphunzitsiyo wanenetsa kuti athana naye.

 

 

Athawa kuotcha tchipisi
Mkulu wina wathawa kuotcha tchipisi pa sitolo zakwa Mbuye-Dziko kwa Kalumo m’boma la Ntchisi. Nkhaniyi ikuti pasitolozo pali mwamuna wina yemwe wakhala akuchita geni yootcha tchipisi ndipo anali wotchuka kwambiri kamba amagulitsa bwino tchipisicho ndipo amalandiranso makasitomala ake bwino. Ndipo mmodzi mwa makasitomala ake anali mtsikana wina yemwe nthawi zambiri amakhala ali pamalopo kugula tchipisicho ndipo nthawi zina amakongola mosavuta. Koma paja chizolowezi cha nankholowa chifumbulutsa mbatata mkulu watchipisiyo ngakhale ali pa banja anadyerera maso pa mtsikanayo. Apo ubwenzi unayamba pakati pa awiriwo. Chibwenzicho chitafumbira mkuluyo anayamba kumafika kwao kwa mtsikanayo ngakhale masana. Tsono tsabata yatha mai amtsikanayo adamwalira ndipo ataika maliro pakhomopo padatsala agogo wina komanso mtsikanayo. Ndipo dzana laliwisili mkuluyo anafika pasiwapo ngati akudzakhuza koma nkuti panthawiyo gogoyo atachoka ndipo panali bwenzi lakeyo basi. Apo awiriwo adayamba kuchita zadama mnyumbamo pamalo omwe adagonekapo thupi lamalemu mai amtsikanayo. Koma awiriwo ali mchikondi gogo uja adangoti balamanthu kulowa mnyumbamo. Gogoyo sanachitire mwina koma kulira ngati kwagwa maliro atapeza awiriwo ali mchikondi. Mosakhalitsa anthu anali ngati fumbi pasiwapo ndipo anayamba kuwowoza awiriwo. Nkhaniyo ataitengera kwa nyakwawa ya mderalo mkuluyo waulura kuti amachita zadamazo pamalo omwe panagona chitandacho pofuna kukhwimila geni yake ya tchipisi atatenga zitsamba zina kwa ng’anga ina ku Mozambique. Ndipo nyakwawa yederalo yalamula mkuluyo kulipira chindapusa cha 1- thousand 5 hundred kwacha. Pakdali pano mkuluyo sakuoneka pamalo ake otchela tchipisi.

 

Mnyamata wamajumbo apenga

Mnyamata wina wogulitsa majumbo kwa Chidothe kwa Mulumbe m’boma la Zomba wapenga. Nkhaniyi ikuti mnyamatayo kwa zaka zambiri wakhala akuchita geni yogulitsa majumbo koma geniyo siimayenda. Apo iye adaganiza zokapempha zitsamba kwa n’ganga ina mderalo. Izi zinachitikadi ndipo wazisambayo adamuuza mnyamatayo kuti chizimba chake ayenera kugona ndi mchemwali wake. Mnyamatayo atafika kwao adayamba kuvutitsa mchemwali wakeyo yemwe ndi wa zaka zisanu. Koma mtsikanayo anadabwa ndi nkhaniyo ndipo adaulula nkhaniyo kwa mikoko yogona pa mudzipo. Apo mikoko yogonayo inakonza kuti imufunse mnyamatayo za nkhaniyo koma iye atadzindikira kuti madzi achita katondo wathawa pamudzipo. Koma anthu ena mderalo akuti dzulo amuona mnyamatayo pa sitolo zina mderalo akuyenda opanda kabudula komanso kutola zam’bini zomwe zikutanthauza kuti mnyamatayo wapenga poti walephera kukwanilitsa zizimba.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter