19/06/17

Written by  Newsroom

Kuponi iwutsa mapiri pa chigwa

Kuponi yolandilira mbeu ndi feteleza zotsika mtengo yautsa mapiri pa chigwa pa mudzi wa Makuta kwa Kalembo m’boma la Balaka. Nkhaniyi ikuti masiku apitawa kunabuka mkangano ku banja lina pa mudzipo.

19
June

Nyakwawa inaitana anthu ake pa mudzipo ndikuwalandiritsa makuponi wogulira fetereza ndi mbeu zotsika mtengo. Banja lina analipatsa kuponi imodzi yoti agulire thumba la fetereza wolemera 50 kilogrammes komanso ina yogulira mbeu. Ndipo malinga ndi kuchepa kwa makuponiwo nyakwawayo inalamula mabanja awiri omwe ndi pachibale kuti agawane fetereza ndi mbeu zotsika mtengo zomwe agule ndi makuponiwo. Koma modabwitsa anthu onse mai wina waku bere lalikulu anakana kugawa fetereza komanso mbeu ndi mchimwene wake wa bere laling’ono. Ndipo mai amene anakana kugawana mbeu ndi fetereza zotsika mtengo ndi mchimwene wakeyo modabwitsa onse walodzanso mbale wakeyo. Tsiku lotsatira anthu pa mudzipo anadabwa kuti munthu yemwe sanampatse gawo la mbeu ndi feterezayo watuluka chotupa ku malo wosayenera. Ndipo munthuyo akulephera kuyenda kotero kuti ali chigonere. Anthu ambiri pa mudzipo omwe akuidziwa nkhaniyi adandaula kwambiri malinga ndi zomwe mai wakadukayo wachita.

 

Mlonda akunthidwa

M'boma lomwelo la Balaka mlonda wina yemwe amagwira ntchito pa chipatala china m’bomalo amukuntha mpaka thapsya kamba kodyelera maso pa mkazi wa mwini. Nkhaniyi ikuti mai wapa mudzi wina kwa Chanthunya anamva mthupi ndipo anapita ku chipatalacho kuti akalandire thandizo la mankhwala. Madokotala atamupima anamuuza kuti amugoneke m’chipatalamo kuti amuonere pafupi. Ndipo pakutha pa masiku awiri mkaziyo anapeza bwino ndipo anamuuza kuti atuluka m’chipatalamo tsiku lotsatira. Koma pamene mkaziyo amawaya-waya kunja kwa chipatalacho kudikilira kuti amutulutse anagwa mchikondi ndi mwamuna wina wolondera pa chipatalacho. Pamene mwini mkaziyo amafika pa chipatalacho kukazonda matenda anapeza mkazi wakeyo akuseka chikha-khali ndi mlondayo apo mwini mkaziyo sanafunenso umboni wina koma kukuntha mlondayo. Pamene anthu ena amaleletsa nkhondoyo nkuti mlondayo magazi akuyendelera mphuno ndi mkamwa. Anthu ena anamutengera mwamuna wa Nsanje ku polisi komwe akayankhe mlanndu wovulaza munthu.

 

Mphunzitsi wamkulu aba ufa wa soya

Mphunzitsi wamkulu wapa sukulu ina kwa Likoswe mboma la Chiradzulu akukhala mwa mantha anthu am’mudzi atamutulukila kuti akumaba ufa waphala la soya. Watitumizila nkhaniyi wati kwanthawi amai ophika phala pa sukuluyo akhala akudandaula ndi zomwe mkuluyo wakhala akuchita nthawi zambili m’malo mopereka matumba okwanila aphala pa tsiku amapereka ochepa koma akamalemba m’mabuku amaonetsa ngati wapereka mlingo oyenelela. Komanso china mchakuti akumadzitenda kukhala dolo kwambili malinga nkuti amauza amai odzaphika phala kuti adzifika past 4 m’mawa koma chodabwitsa mchakuti mphunzitsi wamkuluyo amadzuka past 5 m’mawa omweo koma amakalipila amaiwo ngati antchito ake chonsecho amagwila ntchito modzipereka. Masiku apitawa anthu anamuwendelela pomwe zinadziwika kuti matumba ena a ufa wa soya akumagulitsa. Pa chifukwa-chi nyakwawa, mafumu ndi akulu akulu ena am’mudzi anapita pa sukulu-yo komwe achenjeza kuti akhaulitsa mphunzitsi wamkuluyo yemwe akukhala ngati wamuyaya pa sukuluyo. Mwa zina akulu akuluwo adandaula kuti ana akumadya phala la madzi madzi kwambili chifukwa cha dyela la munthu m’modzi. Panopa, mphunzitsiyo akukhala ndi nkhawa zitamveka kuti akulu akulu am’mudzi ozungulila sukuluyo akukonza zomusamutsa okha.

 


Azimayi awiri aona malodza atasiilidwa maliro okha

Amai awili kwa Khamula mboma la Phalombe aona mbwadza atawasiila okha malilo a malume ao komanso kuti adye okha chakudya pa siwa. Nkhaniyi ikuti amai awiliwo omwe ndipa chibale samakonda kupita m’malilo ndipo akapezeka kuti apita ku malilo amakanitsitsa kudya chakudya ati ponena kuti sadya m’malilo. Koma mwatsoka tsiku lina malume ao anamwalila ndipo pa chifukwa-chi anthu anafika pa siwa mwaunyinji ndipo zonse zinayambika bwino. Ophika amai amagwila ntchito chimodzi modzinso adzukulu kumanda. Koma nthawi ya chakudya amai anapakula msima ma beseni anai ndipo onse anakasiila anamfedwawo awiliwo ati kuti iwakwane podziwa kuti ati samadya kumalilo. M’modzi mwa amaiwo anakhalila koma koma sizinaphule kanthu malinga nkuti nzake anamuthawa. Kupita kumanda nako adzukulu anakana kukwilila malilo ndipo anapatsa mai wotsalayo kuti akwilile yekha malilo amalume ake. Mayiyo anayambadi kugwila ntchitoyo kufikila ampingo anamuthandiza. Tsiku lotsatila posesa nyakwawa inalangiza anthu m’mudzimo kuti atengere phunzilo pa zomwe zinachitikazo. Panapo zamveka kuti amai onse awili ayamba kupezeka m’malilo ochitika m’mudzimo ngakhale akumayenda ali wela wela ngati ataya singano chifukwa cha manyazi.


Login Form

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter