Ayenda mwamanyazi mbiri yawo itawanda
Mnyamata wina kwa Iwala ku Ntaja m’boma la Machinga akuyenda zamadulira atazindikira kuti mbiri yake yawanda yofuna kulanda katundu wa m’nyumba ya mchemwali wake.
Mbava itupa mimba kamba kokuba mbuzi
Mbava ina kwa Mbera m’boma la Balaka ili pa ululu woopsya itatupa mimba chifukwa chakuba mbuzi ya mai wina mderalo.
Ukwati utha kamba ka chimasomaso
Mayi wina kwa Kanduku mboma la Mwanza akunong’oneza bondo mwamuna wake atamuuza kuti ukwati watha chifukwa cha khalidwe lake la chimasomaso.
Mayi okonda zopemphera agwidwa akuchita zadama
Mayi wina wodziwika bwino ndi nkhani zopemphera ku Urongwe mboma la Balaka wakhumudwitsa anthu atagwidwa akuchita zachisembwere kunja kutachita kachisisila chakumadzulo mtchalichi ina yomwe iye sapempherako.