Azimayi atatu awilikiza uhule
Anthu aku Mbayani mu mzinda wa Blantyre akuti aimika manja m’mwamba chifukwa cha zomwe amai atatu apa banja akuchita powilikiza za uhule ndi amuna apa banjanso.
Akolola chimanga cha eni
Anyamata ena awiri kwa Kwataine m’boma la Ntcheu awakwidzinga atawagwira akukolola chimanga m’munda wa mwini.
Akuchimuna akana kupita kuukwati
Makolo a mnyamata wina ku Misesa kwa Kapeni mboma la Blantyre amenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti sadzapita ku ukwati wapa tchalitchi wa mwana wao wa mwamuna kumapeto a mwezi uno chifukwa choti akuchikazi akuyendetsa okha zokonzekera zonse za chisangalalo-cho.
Mtsikana oyendayenda atibulidwa pamaliro
Mtsikana wina oyendayenda m’mudzi wa Kapichi m’boma la Thyolo amutibula mpaka kukomoka pa mwambo wamaliro.