16/04/15

Written by  Newsroom

Awona polekera kuchita zachimasomaso
Bambo wina wachimasomaso kwa T/A Chimombo mboma la Nsanje aona polekera atagonana ndi mtsikana yemwe bamboyo amayembekezera kuti aperekeze mdzukulu wake pokafunsila ukwati.

16
April

Nkhaniyi ikuti mnyamata wina yemwe amagwira ntchito za kabaza anapeza mkazi woti amange naye ukwati, koma osadziwa kuti mtsikanayo anali oyendayenda. Anthuwo anagwirizana zoti malume a mnyamatayo akaonekere kwa mtsikanayo ndipo patadutsa masiku ochepa anapereka chithunzi kwa msungwanayo ngati njira imodzi yoti adzimukumbukira. Poti wachake ngwachake mtsikanayo anapita kukachezetsa alendo ku boma , apa ndi pamene anakomana ndi atsibweniwo nawonso akuyang’ana munthu woti awasangalatse pokhala kuti iwo anali achakumwa wapa malopo. Anthuwa awiriwa anayamba kumwa mowa mpaka mtsikanayo analedzera kwambiri ndipo anapita ku malo ogona. Mbandakucha Mtsikanayo anatsanzika bamboyo kuti akukataya madzi koma mphono salota anasiya chikwama chake, ndipo bamboyo anayamba kuyang’ana mchikwamamo, koma anayima mutu atapeza chithunzi cha Mdzukulu waoyo, ndipo chisangalalo chinathera panjira koma atagona naye kale, koma sanamufunse chili chonse. Pokafunsa mdzukulu waoyo za maonekedwe a msungwanayo anawafotokozera ndendende ndi momwe aliri ndipo iwo anasowa cholankhula. 

 

Bambo avala dilesi posangalala kuti mkazi wao ali ndi pathupi
Anthu a ku Chilobwe mu mzinda wa Blantyre ndiokhumudwa pamene ena anafa ndi chikhakhali poona bambo wina akungoyendayenda usiku atavala dilesi komanso ndolo ati posangalala kuti mkazi wake ali ndi pathupi. Nkhaniyi ikuti banjalo lakhala likufuna mwana kwa nthawi yayitali, komabe zimavuta kuti akhale ndi mwana. Anthu m’deralo akhala akuwalangiza kuti zonse ndi zotheka ndi Ambuye ndipo chimene anagachite nkudikirila kwa Chauta. Tsiku lina ali mkati kucheza, mwamunayo anaona ngati kutulo Mkazi wake atamuuza kuti mayio ali ndi pathupi. Apa bamboyo anadzambatuka, kuyamba kuvina kosalekeza kwinaku akululutila chifukwa cha nkhani yokomayo. Koma chodabwitsa nchakuti Mkaziyo anadzidzimuka ataona bamboyo akuvala dilesi ndi ndolo ati popitiliza chisangalalacho kenako anasowa mnyumbamo ndikuyamba kuyendayenda usiku. Anthu m’deralo adzudzula bamboyo ponena kuti, chimenechi sichisangalalo koma ziwanda.

Get Your Newsletter