15/04/15

Written by  Newsroom

Azimayi ajuga aphwanyisa mnyumba ya mzawo
Anthu okhala ku Area 9 ku Machinjiri mu mzinda wa Blantyre ndiokhumudwa chifukwa cha zomwe achita azimayi ena otchova juga pomphwanyisa nyumba ya mzawo.

15
April

Nkhaniyi ikuti azimayi ena mderalo ali ndi khalidwe lotchova juga amunawo akachoka kupita ku ntchito, koma anthu okhala moyandikana ndi azimayi akhala akuwadzudzula pa khalidwe lao lochititsa manyazilo. Poti amati wachake ngwachake lero kumasanaku anapitilizabe ndi khalidwe lawo pafupi ndi nyumba ina ya mzawo. Ali mkati pa wachiona ndani m’modzi mwa mayi omwe amachita nawo jugayo mamuna wake anatulukira mwadzidzi pa malopo atatsinidwa khutu pa zomwe amayiwo amachita koma ataledzera kwambiri. Apa sanachedwe koma kuyamba kuphaphalitsa amaiyo ndi makofi ndipo amayiyo ataona kuti akuchepera anatola miyala ndi zinthu zina kugendera bamboyo mpaka magazi ku mkhope ndi m’mutu. Apa nayenso sanayimve mpaka anamenyana ndi azimayiwo omwe anathawira mnyumba yoyandikana nayo ya mzawoyo kutseka kuchitseko pamene mwini nyumba kulibe. Bamboyo pokhala akuti anali atamwa kabanga anayamba kuphwanya magalasi a nyumbayo uku akuzazila azimayiwo ponena mokuwa.. tulukani tithane panja pano. Mtolankhaniwathu pamene amachoka pa malopo nkuti anthu a mderalo akufunafuna akuluakulu a mderalo kuti awone chochita ndi bamboyo komaso azimayiwo.

Anthu afa ndi phwete mu minibus
Tili ku Machinjili komweko anthu omwe anakwera minibasi ina mu msewu wa Nkolokoti kuchokera ku Limbe anafa ndi mphwete pamene bambo wina yemwe analedzera koma anakwera mpando wakutsogolo atamang’ala kwa kondakitala pamene amatsika minibasiyo kuti ambwezere theka ya ndalama yomwe analipila ati ponena kuti basiyo theka ina ya ulendowo sinagwiritse ntchito mafuta a galimoto. Nkhaniyi ikuti bamboyo amachita chidwi ndi zomwe amachita dalaivala pamene amazimitsila galimotoyo pafupipafupi mchingerezi amati nuatral monga momwe amachitila akakhala pa mtsetse. Mkuluyo mu njira yonseyo sanalankhulepo kanthu, koma pamene amatsika anafunsa dalaivalayo kuti KODI PAMENEPA TINENE KUTI MWAONONGA MAFUTA NGATI? Apa dalaivalayo anangoseka nanena kuti kuiongolera, apa ndi pamene anayamba kuvuta kuti ambwezere ndalama. Poona kuti bamboyo akuchedwetsa anthu, ena anamukokera pa mbali ndipo basiyo inanyamuka pa liwiro la mtondo wodoka. Mkuluyo anamusiya pa sitejipo koma akulalata kuti ndakudziwani.

Zinthu zowuluka zisautsa anthu
Anthu omwe akukhala pa msasa wina chifukwa cha madzi osefukira kwa TA Mwambo mboma la Zomba ati ndiodabwa ndi zinthu zina zokhala ngati zouluka koma zosadziwika zikumabwera usiku uliwonse kudzavutitsa anthuwo akafuna kukagona. Malingana ndi m’modzi mwa anthu ozungulira pa malopo ati anthuwo afika posowa mtendere ndi zinthuzo.

Get Your Newsletter