14/04/15

Written by  Newsroom

Mbava yaikazi ikanidwa kulowa mu golosale
Mai wina kwa TA Msamala mboma la Balaka amuletsa kuti asadzalowenso mu golosale ya banjalo mwamuna wake atazindikira kuti mayiyo ndi mbava.

15
April

Nkhaniyi ikuti banjalo linatsegula golosale komanso limalimbika pa ntchito zakumunda moti chaka chilichonse amakolola chimanga chambiri. Pachifukwachi mayiyo anayamba kuzembetsa katundu osiyanasiyana kuphatikizapo chimanga ndi ndalama nkumakapereka kwa makolo ake koma makolowo samadziwa kuti mwana waoyo akuchita kuba zinthuzo. Tsono chavumbulutsa mavu pa chisa nchakuti mayiyo anaba foni ya nzake oyandikana naye nyumba nkukamupatsa mwana wake yemwe amaphunzira pa sukulu ina ya Private mbomalo. Mwini foniyo atayiona anayizindikira ndipo atamufunsa mwanayo anaulula kuti amugulira ndi mayi ake. Apa zinthu zinafika povuta chifukwa atamutenga mwanayo kukamufunsa za foniyo pamaso pa mayi akewo anangoti kakasi kusowa choyankha. Mwamuna wake atamva za nkhaniyi mpamene anazindikira kuti mayiyo wakhala akumubera katundu osiyanasiyana komanso ndalama za mgolosale nkumakapereka kwa makolo ake. Panopa mwamunayo wakwiya kwambiri ndi nkhaniyi ndipo wamuchenjeza mkaziyo kuti asadzamuonenso akugulitsa ngakhale kulowa m’golosalemo.



Avulaza apolisi
Apolisi akufufuza anthu ena ku Tchoda mdera la Mfumu Nkalo mboma la Chiradzulu pa mlandu womenya ndikuvulaza apolisi ena omwe amagwira ntchito mderalo. Ofalitsa nkhani za apolisi mchigawo chakumwera Nicholas Gondwa wati apolisi omwe avulalawo ndi Constable Mkwezalamba ndi Constable Kalenje omwe amagwira ntchito yolimbana ndi mchitidwe wotentha makala ndipo anakomana ndi zaupanduzi pamene amafuna kulanda makala kwa anthu ena awiri. Ali mkati molimbana ndi anthuwo, anthu ena anayamba kulimbana ndi apolisiwo mpaka kuwamenya modetsa nkhawa. Malipoti ati m’modzi mwa apolisiwo anamulanda mfuti koma apolisi anaipeza tsiku lomwelo. Pakadai pano ntchito yofufuza anthu omwe adamenya apolisiwo ili mkati.


Apha mayi wa pathupi ndikuchotsa mwana
Khothi lina mboma la Mwanza lachitatu lapitali lidapeza olakwa banja lina lomwe linapha mayi wina yemwe anali ndi pathupi ndikuchotsa khandalo. Zimenezi zidachitika m’ mwezi wa September mchaka cha 2004 mbomalo pamene banjalo linanyengerera mayiyo kuti atsagane naye ku mtsinje wina. Mai Stornia Benard omwe akuwazenga mlanduwo pamodzi ndi mwamuna wawo akhala akunamiza anthu kuti ndi woyembekezera ndipo patsikulo ananamizira ngati akachilira ku mtsinjeko komwe anabwerako ndi khandalo. Azachipatala atafufuza mpamene anapeza umboni woti mai Bernard sanali woyembekezera. Apolisi mbomalo ati khothilo kupyolera kwa Jaji Rowland Mbvundula lidzapereka chilango pa mlanduwo pa 24 mwezi uno.

Get Your Newsletter