Poyamba mnyamatayo akuti anali wokhulupirika kwa mkazi wakeyo koma masiku apitawa zinthu zinayamba kusintha pomwe anapeza chibwenzi m’mudzi oyandikana ndi kwawoko. Ndiye poti amati ukatambatamba uziyang’ana kunja kuopa kuti kungakuchere, mnyamatayo anatayilira mpaka mphekesera inamupeza mkazi wakeyo. Mkaziyo analephera kuugwira mtima mpaka anapita kwa chibwenzicho kukafunsa za nkhaniyi. Mayiyo anakwekweza nzakeyo kuti akafunse nkhaniyi pamaso pa mwamuna wake ndipo atafika mwamunayo anachita tsemwe. Posakhalitsa mkangano unayamba ndi mwamuna wakeyo mpaka kuyamba kumenyana ndipo kenaka anayambanso kukunthana ndi mkazi nzakeyo koma mwa mwayi anthu ena a m’mudzimo analeretsa ndeuyo. Pakadali pano mnyamatayo akukhalabe limodzi ndi mkazi wakeyo komabe mkaziyo akuonana ndi diso la nkhwezule ndi mayi wakubayo ndipo sizikuziwika ngati chibwenzicho chipitilire kapena ayi.
Agona ndi akazi awiri pa bedi imodzi
Mkulu wina waimitsa mitu mikoko yogona kwa Mondiwa ku Bangwe mu mzinda wa Blantyre atamutulukila kuti akukhala ndi akazi awili nyumba imodzi mpaka kumagona pa bedi limodzi. Nkhaniyi ikuti m’nyamata wina adauza mkazi wake kuti ati kwabwela wachibale wakumudzi kwao koma ndi wa mkazi ndikuti azikhala kunyumbako. Poyambilila mlendoyo akuti amagona pabalaza koma atatha mwezi akuti mwamuna wa m’nyumba muja anauza mkazi wake kuti tsopano mlendo uja azigona nao ku chipinda chifukwa pabalaza pakumadontha chifukwa cha Mvula. Atayamba kugona kuchipinda mlendo uja akuti amanyinyilika kugona pansi mpaka tsiku lina anagona nao pa bedi paja. Mkazi wamkuluyo akuti anamuopsyeza kuti akanena kunja za nkhani-yi amupititsa kumudzi. Panopa, zadziwika tsopano kuti mwamunayo akumagona ndi akazi onse awili bedi limodzi ngati banja. Malinga ndi amene watumiza nkhaniyi mkuluyo amanama kuti mkaziyo anali m’bale wake wakumudzi koma ali bwenzi lake lakalekale. Panopa, mkazi wamkuluyo akuoneka kuti sakukondwa ndi nkhaniyi koma mwina akula ndi mantha kuti amupititsa kumudzi.
Azicheka pamimba chibwenzi chitathetsa
Mtauni yomwe-yo ya Bangwe mu mzinda wa Blantyre mwamuna wina akulila mchipatala atazicheka pa mimba mpaka matumbo pa mtunda ati chifukwa choti bwenzi lake linamuuza kuti chibwenzi chatha. Nkhaniyi ikuti m’nyamata wina anali pa chibwenzi ndi mtsikana wina ndipo chibwenzi chao chinali chosililika. Ngakhale mkaziyo anali pa chibwenzi ndi m’nyamatayo samadziwa kuti ati anali pa banja kale. Choncho atazindikila za nkhani-yi anathetsa chibwenzicho dzuwa likuswa mtengo. Koma akuti mwamunayo sadaimve nkhani-yi ndipo m’malo mwake anapita kwa mkaziyo ndikumubaya ndi mpeni nkuthawila kunyumba kwao komwe anakazicheka pamimba mpaka matumbo pa mtunda. Mwa mwai akuti onse awili anathamangila nao ku chipatala komwe akuti mwamunayo akubuulilabe ndi ululu wa bala lapa mimbalo pamene mkaziyo zikumveka kuti amutulutsa. Pakadali pano nkhani ndi yake pa laini pomwe amakhala pamene zikumveka kuti apolisi akudikila kuti apeze kaye bwino ncholinga choti akayankhe mlandu.