10/04/15

Written by  Newsroom

Abwenza ndalama poopa kulandidwa katundu
Mkazi wina yemwe mwamuna wake adamwalila posachedwapa wabweza ndalama kwa mwamuna wina yemwe amamuyenda njomba poopa akuchimuna kuti amulanda katundu kwa Mayaka mboma la Zomba.

15
April

Nkhani-yi ikuti mkazi wina mwamuna wake anamwalila ndipo poopa kuchedwa akuchimuna kumusudzula akuti anayamba kuyenda mwanseli ndi mkulu wina wogulitsa nsapato mpaka chibwenzi chao chinafumbila. Mosakhalitsa mayiyo akuti anapalananso ubwenzi ndi mphongo ina mpaka kumayendetsa chiwili. Momwe amachita zimenezi akuti amayesetsa kuti amuna awiliwo asadzakumane poopa mapokoso kuti akuchimuna adzawadziwa. Komabe poti paja amati tsiku la fote likakwana amuna aja anakumanizana koma mwai unali woti mwamuna m’modzi anali odekha kwambili koma anauza mayiyo kuti amubwezele ndalama zake. Mayiyo akuti anafuna kuyamba kulimbalimba koma zinakanika kamba koti mkuluyo anamuuza kuti akatula nkhani-yi ku bwalo. Pa chifukwachi mayiyo akuti wabweza ndalama yonse 14-Thousand 4 hundred zomwe anamupatsa masiku apitawa. Mayiyo akuti anachita zimenezi poopa akuchimuna kuti mwina atha kumulanda katundu kuti wayamba kuwilikiza khalidwe la mchiuno. Koma malinga ndi amene watitumizira nkhaniyi akuchimuna aja alandila kale nkhaniyi ndi chidwi kwambili ngakhale ena akuwadzudzula kuti achedwa kumusudzula mayiyo.



Alipira nkhuku kamba konyezesa nyakwawa
Mayi wina ku Chigumula mu mzinda wa Blantyre amulamula kuti apereke chindapusa cha nkhuku ziwiri ku bwalo komanso K1000 kwa odandaula chifukwa chonyozera zomwe inalamula nyakwawa ya m’mudzimo pomuitanitsa mayiyo ku bwalo. Nkhaniyi ikuti mayiyo adagula malo kwa mkulu wina m’deralo ncholinga choti amangepo nyumba komanso mbali ina ikhale munda. Mayiyo akuti wakhala pamalopo kwa zaka zisanu nzitatu ndipo zonse zimayenda tayale. Tsono chomwe chachitika nchoti mbale wina wa mayiyo adagulanso mbali ina ya malowo ncholinga choti azilima. Mayiyo ataona izi akuti anayamba kubyala mitengo m’malire ndi nzakeyo koma vuto ndi loti analowelera malo a nzakewo. Chinaso nchakuti nzakeyo anapeza chimanga pafupifupi makumi atatu chitathyoledwa m’mundamo pomwenso amaganizira kuti anathyola ndi mayiyo. Apa mkangano waukulu unabuka pakati pa amayi awiriwa mpaka kufuna kuundana m’dothi. Nyakwawa ya m’mudzimo itamva nkhaniyi inayitanitsa amayi onsewo ku bwalo kuti akafotokoze bwino za mkanganowo koma mayiyo akuti sanapiteko ku bwaloko ponena kuti ati anatopa kukamba milandu yokhudza malo. Pachifukwachi nyakwawayo inalamula mayiyo kuti apereke chindapusacho ngati cha bwalo komanso one thousand kwacha ngati chipepeso kwa nzakeyo.

Get Your Newsletter