Nkhaniyi ikuti kumeneko kuli mkwambiwini wina yemwe anakwatira mbumba ina ndipo wakhala pa banjapo zaka zoposa zisanu. Ndipo banjalo limakhala bwino popeza mwamunayo anali wodzilimbikira monga kulima komanso kuchita malonda osiyana-siyana. Koma ngakhale zinali chomwecho Mulungu sanawadalitse awiriwo ndi mphatso ya mwana. Apo eni mbumba anaitanitsa mkazi wa banjalo ndikumulangiza kuti athamngitse mwamunayo popeza walephera ntchito yake yochulukitsa mbumbayo. Mkaziyo ngakhale sanakhutire ndi ganizo la malume akewo wathamangitsadi mwamuna wakeyo koma monyinyitka. Anthu mderalo ati akhumudwa kwambiri ndi nkhaniyi kamba ana ndi mphatso yochokera kwa Mulungu ndipo ati iwo sakudziwa kuti pakati pa mwamuna ndi mkaziyo chumba ndi ndani? Komanso anthuwo adandaula kamba koti makolo omwe athetsa banjawo amalimbikira kutumikila kumpingo kwao.
Anthu akhala mwa mantha kamba ka mzukwa
Anthu akukhala mwa mantha mdera la m’boma la Blantyre kamba ka mzukwa omwe ukumaoneka mdelalo. Yemwe watumiza nkhaniyi wati kumeneko kunali mkulu wina yemwe anamwalila atagwela pamadzi. Nkhani ikuti mkuluyo adapita ku dziwe lina kukacha kumeneko koma kenaka adasiila mkazi wake ntchitoyo ponena kuti amafuna asambile pa dziwelo. Koma atagwela pa dziwepo anayamba kusambila koma mwatsoka anamila ndipo apa mkazi wake anaitana anathu kuti amuthandize kumpulumutsa koma sizidaphule kanthu. Ntchito yofuna thupi la mkuluyo idatenga masiku atatu ndipo lachinayi lake adapeza thupilo likuyandama. Mwambo onse wamalilo udachitika bwino lomwe nghakhale anthu ena mdelalo amakaikila momwe mkuluyo adafela. Panopa tsopano zadziwika kuti anthu amdela lomwe mkuluyo amakhala ali ndi mantha kwambili malinga nkuti akumakumana ndi mkuluyo m’malo osiyanasiyana kuphatikizapo ku mitengo ya gwafa mdelalo. Pakadali pano, eni mbumba ati aponda –ponda kuti apeze chomwe chinapha m’bale wawo-yo.
Mnyamata wina adabwisa anthu pa maliro
Mnyamata wina wadabwitsa anthu pamaliro a bambo ake mdera la Kaphuka m’boma la Dedza. Yemwe watumiza nkhaniyi wati kumeneko kunali mkulu wina yemwe anadwala kwa nthawi yaitali ndithu. Ngakhale achibale ake anayetsera kuponda apa ndi apa zinthu zinakanika mpaka bamboyo anamwalira. Apa mikoko yogona inamema anthu kuzakhazika anamfedwa pasiwapo malinga ndi mwambo wa Maliro kumeneko. Anthu ali pasiwapo anali odabwa kuona mwana malemuyo atakwera ya denga la nyumbayo koma ali ndi madzi mkachipande. Anthu omwe anali pasiwapo atamumfutsa iye anayankha m’maso muli gwa kuti akufuna kusambitsa mtembo wa abambo akewo monga momwe adamulangizila asanamwalire. Pamenepa, iye anapitiliza kuti ngati satero anthu pakhomopo atha m’modzi m’mnodzi psyiti. Pakadali pano anthu mderalo ati ndi odabwa ndi zomwe anachita mwanayo ndipo akukhala ndi chidwi kuti aone momwe zither ndipo anthu ambili nkutheka kuti mnyamatayo amatenga zizimba pa dengalo.
Banja lina liweyeseka
Banja lina laweyezeka mdera la Timbiri m’boma la Nkhata Bay. Yemwe watumiza nkhaniyi wati mdero muli banja lina lomwe mwamuna wake amagwira ntchito ku kampani ina yomwe ili mdera lomwelo. Ndipo tsiku lina bamboyo analawira mkazi wake kuti akupita ku ntchito monga mwa nthawi zonse. Koma pobwera ku ntchitoko mwamunayo sanapeze mkazi wakeyo pakhomo. Ndipo atafunsa anthu ena oyandikana naye nyumba anati sakudziwa komwe mkaziyo anapita pa nthawiyo. Apa bamboyo anapita kumalo ena omwela mowa ati pofuna kutayitsa nthawi. Koma ali komwe-ko anadabwa kuona mkazi wake akutuluka mchipinda china chogonda anthu apa ulendo ali ndi mwamuna wina yemwe ndi mzake weni-weni wa mwamunayo. Pachifukwa-chi mkaziyo anagwetsa nkhope yake pansi ataona mwamuna wake-yo ali pamalopo ndipo anamuchonderela kuti amukhululukire pa zomwe anachitazo. Koma mwamuna wakubayo ataona mwini mkaziyo analiyala liwilo la mtondo wadooka ati kuopa kuti anthu amuphika. Pakadali pano mwini mkaziyo watementsa nkhwangwa pa mwala kuti sakumufunanso mkazi wakeyo chifukwa cha mtima wake osakhutila.