Nkhaniyi ikuti mwamunayo yemwe ndi m’modzi mwa akuluakulu oyang’anila sukulu ina mderalo wakhala ali pa ubwenzi wa ntseri ndi mai wina yemwe ndi mkazi wa mwamuna wina ogwira naye ntchito pa malopo. Chodabwitsa kwa nthawi yayitali mwamuna wa mkaziyo wakhala asakudziwa za ubwenziwo kufikira anthu ena atamutsina khutu pa nkhaniyi. Paja pali mau oti lafote limakwana tsiku lina anthu ena apa sukulupo anapezerela maiyo ndi bwanayo ali buno-buno. Apa anthuwo sanachedwe koma kukauza mwini mkaziyo. Mwini mkaziyo pamodzi ndi anthuwo anathamangira ku maloko ndipo kunali kumenya kolapitsa uku ena atathamangira kunyumba ya bwanayo ndikuswa ena mwa magalasi a nyumba yake potengera mwai kuti bwanayo ndi omva zayekha ndipo wakhala akuzunza anthu ogwira ntchito pa sukuluyo. Koma zomvetsa chisoni mkazi wa mwamunayo anauza mwamuna wakeyo kuti sakumufunanso komanso kumuuza kuti ana omwe ali nawo ndiya bwanayo. Chimene chaimitsa mitu ya mikoko yogona m’deralo komanso anthu ambiri mchakuti mwamunayo wabwerela kuchokera kwao komwe anapita ndikuyamba kuchonderela mkazi wake kuti abwerelane. Pakadali pano anthu ambiri ati mwina nkutheka kuti mwamunayo anamudyetsa mchira wa buluzi.
Mai wina agwidwa njakata
Mai wina mdera la Malemia m’boma la Nsanje manja ali ku nkhongo atalandila telefoni kuchokera kwa mwamuna wake yemwe ali ku Joni. Nkhaniyi ikuti miyezi ingapo yapitayi maiyo anawilikiza kuyenda ndi amuna a weni ngakhale anthu ambiri akhala akumudzudzula koma maiyo wakhala akuponyera ku nkhongo malangizowo. Maiyo yemwe akukhala ku chitengwa wakhala akuchenjezedwa chifukwa cha nkhaniyi koma wakhala akuyankhula mosimbwa kuti palibe yemwe angamuuze chochita. Pa chifukwachi abale a mwamunayo akhala asakukondwa ndi zomwe amachita maiyo ndipo anaimbira foni mchimwene waoyo ndikumufotokozera tsatane-tsatane wa nkhaniyi. Apa mwamunayo sanayankhe msanga koma kufufuza kudzera mu njira zina zosiyana-siyana ndipo kumapeto kwake anakhutitsidwadi kuti zomwe wakhala akumvazo ndi zoona. Mwamunayo masiku apitawa aimbira foni mkaziyo komanso kumulembera kalata kuti banja latha. Pakadali pano maiyo manja ali nkhongo chifukwa mwa zina mwamunayo wamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti sabwerela mbuyo pa nkhaniyi. Maiyo akungokhalira kuzungulirazungulira pa boma la Nsanje.
Dokotala wina apulumuka kwa wamisala wampeni
Dokotala wina pa chipatala china m’boma la Zomba wanenetsa kuti sadzayerekeza pa moyo wake kusiya kutamanda Mulungu. Nkhaniyi ikuti masiku apitawa dokotalayo ali pa ntchito yake mu ofesi mwadzidzi munalowa munthu wina wamisala. Apa dokotalayo anali ndi mantha aakulu potengera kuti wamisalayo anali ndi mpeni m’manja ndipo posakhalitsa anaophyesa dokotalayo. Dokotalayo zinamukoka manja mpaka kugwada pansi uku akunjenjemera ndi pemphero la malilime. Chosangalata wamisalayo anauza dokotalayo kuti adzuke ndipo anapereka mpeni uja kwa mwamunayo koma dokotalayo sanamvetse. Kumapeto kwake wamisalayo anauza dokotalayo kuti akhoza nayenso kumuthamangitsa zomwe zinapangitsa kuti dokotalayo kuti asowe choyankhula. Anthu ambiri pa boma la Zomba omwe amaona izi zikuchitika anauza mwamunayo kuti mpofunika kuti adzipemphera kwambiri chifukwa zomwe zachitikazo mchifukwa choti mzimu wa Ambuye unali mbali yake. Pakadali pano mwamunayo wanenetse kuti sadzayerekeza pa moyo wake kusiya kumvera Mulungu.
Nyakwawa ina ithidzimulidwa
Nyakwawa ina mdera la Makanjira m’boma la Salima inalira ngati kwagwa maliro ataithidzimula kwa chakwanu leka. Nkhaniyi ikuti nyakwawayo yakhala ikudzudzulidwa chifukwa chaza khalidwwe lake losokoneza mabanja a weni. Anthu akaidzudzula nthawi zambiri yakhala ikuyankha motumbwa kuti iyo ndi mlelakhungwa choncho iyo ntchito yake nkusamala anthu. Pa chifukwachi anthu ambiri akhala asakukondwa ndi makhalidwe a nyakwawayo potengera kuti imaoneka kuti ndi nsavankunkhu chikhalireni anthu ambiri ali ndi maumboni osiyana-siyana pa nkhaniyi. Masiku apitawo nyakwawayo inapita kunyumba kwa mai wina yemwe ali naye pa ubwenzi wa tseri poganizila kuti mwamuna wa maiyo yemwe ndi nsodzi anali ali kunyanja. Mphuno salota pamene nyakwawayo imafika pakhomopo, mwini mkaziyo anali mnyumba ndipo mofulumira anagwira nyakwawayo ndikuyamba kuithidzimula mpakana kulira ngati kwachitika maliro. Chifukwa cha mfuu anthu ambiri anakhamukira kunyumbako ndipo kunali kumenya kosayang’ana nkhope koma Nyakwawayo inayesetsa kuchonderela kuti ayisiye koma anthu anapindila ndevu mkamwa. Apa anthuwo anakwakwazila nyakwawayo kwa mfumu ya ndondo ndipo ku bwalo la mfumu nyakwawayo inaona ngati kutulo itauzidwa kuti iyambe yasiya ntchito yake yaunyakwawa. Chifukwa cha kusamvetsa nyakwawayo inakadandaula ku polisi za nkhaniyi koma sizinaphule kanthu. Pakadali pano nyakwawayo ikukhalira kutandala mnyumba chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi.
Anthu ena asiya kupemphera mu mpingo wina ku Phalombe
Mamembala ochuluka a mpingo wina m’dera la Mulomba ku Phalombe asiya kupemphera mu mpingowo. Nkhaniyi ikuti mbuyomu mderalo mwakhala muli mphekesera yoti m’busa wa mpingowo ndi tsinzinamtole otheratu m’malo moonetsa khalidwe labwino ngati mtumiki wa Mulungu. Mwa zina Mbusayo mbuyomu anathamangitsidwapo akuba mondokwa m’munda wa mlimi wina chikhalireni mamembala amu mpingowo amachita chili chonse kuti adzikhala okondwa pamene akutumikira. Masiku apitawa gulupayo anthu ena anamuona akuthyola mati-mati m’munda ndipo anthu ena anakafotokozera mwini mundayo za nkhaniyi. Atakafika kunyumba-ko mwatsoka anapeza kuti gulupayo wapita kokagulitsa tomatoyo ku msika pokhaka kuti inali tsiku la msika. Mikoko yogona komanso anthu ena atafufuza bwino lomwe za nkhaniyi zinadziwika kuti tomatoyo anali obedwa ndipo apa gulupayo anangoti kukamwa yasa kusowa choyankhula. Pamene timalandila nkhaniyi mamembala ambiri amu mpingowo atuluka mu mpingowo ndipo ati sakuonanso chifukwa chobwerelera mu mpingowo. Mbusayo akuyenda njira zodula chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi. Likulu la mpingowo lati lifufuza za nkhaniyi ndipo zoona za nkhaniyi zikadziwika aona chochita ndi Mbusayo.