Nkhaniyi ikuti mphunzitsi wina wapa sukulupo anapalana ubwenzi wa m’nseri ndi mtsikanayo wina wapa sukulupo mpaka kumupatsa pathupi. Nkhaniyi itadziwika, makolo anakamang’ala kwa mphunzitsi wamkulu komanso komiti yoyang’anira sukululo kuti aone chochita pa nkhaniyi. Koma chodabwitsa nchakuti mphunzitsiyo anamusamutsira ku sukulu ina kusiya mtsikanayo ali kakasi kusowa chochita. Nthawi yolemba mayeso itakwana mtsikanayo anamuletsa ponena kuti ati ndi wapa banja. Anthu mderalo akudabwa kwambiri ndi zomwe achita mphunzitsi wamkulu wapa sukuluyo mogwirizana ndi komiti yoyendetsa ntchito zapa sukuluyo ponena kuti akanangomulola mtsikanayo kulemba nawo mayeso. Mikoko yogona pa mudzipo itafufuza bwino za nkhaniyo yapeza kuti mphunzitsi yemwe wapereka pathupi kwa mtsikanayo anapereka chiphuphu kwa aphunzitsi anzake ndi anthu ena kuti nkhani isapite patsogolo.
Apeleka malangizo oyipa kwa mwana wawo
Amai apa mudzi wina kwa Kabunduli mboma la Nkhatabay adzudzula kwambiri mayi nzawo kamba kopeleka malangizo oyipa kwa mwaka wake wa mkazi. Nkhaniyi ikuti mwana wa mayiyo, mabanja ake akhala akutha chifukwa choti mayi ake akhala akumuuza kuti sanafikepo, ati ponena kuti amuna wonse amakomana nawo amaoneka kuti nthawi zambiri amakhala khwakhwakhwa. Pa chifukwa ichi wakhala akuuza mwana wakeyo kuti adzifufuza mwamuna wachuma ati chifukwa choti iwo amafuna mwamuna woti adzimudyera bwino ati chifukwa choti mwana waoyo ndi njole. Mphuto salota mwamuna yemwe wasiyana naye posachedwapa wapezeka kuti zake zayamba kumuyendera ndipo mtsikanayo sanachitire mwina koma anakachonderela mwamunayo kuti abwelerane banja. Mwamuyo watemetsa nkhwangwa pa mwala kuti zivute zitani sakumufunanso mkaziyo kamba koti wazindikira kuti safuna banja koma akuyang’ana chuma. Apa mtsikanayo analira mokweza ngati kwagwa zovuta uku akuyankhula mokweza kuti NDINUYO AMAI ZONSEZI. Mikoko yogona pa mudzipo komanso amayi adzudzula kwambiri mayi nzawoyo chifukwa chochititsa kuti mwana waoyo abwelere m’phala.