12/05/15

Written by  Newsroom

Kazizi tsakamuka kudenga pamapemphero
Mapemphero anasokonezeka mu mpingo wina kwa mfumu Kalonga m’boma la Salima , Kadzidzi wakufa atatsakamuka kudenga nkugwera m’busa yemwe amalalikira.

12
May

Nkhaniyi ikuti kwa nthawi yaitali akulu-akulu ena amu mpingomo akhala akukangana chifukwa cha ndalama zina zomwe anasonkha akhristu mu mpingomo kuti zigwire ntchito za chitukuko koma mkulu wina anazinyambita. Pamenepa m’busa wa mpingowo wakhala akudzudzula mchitidwe wowononga ndalama-wo pomwe anati kunali bwino kuti anthu omwe adaononga ndalamazo achoke mu mpingowo. Koma mauwa sanasangalatse anthu omwe akukhudzidwa ndi nkhaniyi ndipo anachenjeza kuti tsiku lina m’tchalitchimo mudzachitika zinthu za chilendo. Patsikulo m’busayo akulalikira mtchalichimo, Kadzidzi anatsakamuka ndikugwera m’busayo. Nthawi yomweyo m’busayo anafooka zomwe anthu ena akuganiza kuti kadzidziyo anali wamatsenga. Pamenepa mapemphero onse anasokonezeka. Pakadali pano m’busayo wanenetsa kuti sachoka patchalipo chifukwa choti moyo wake amawuteteza ndi chauta koma akhristu ena akuti akhumudwa ndi zomwe anthu ena akuchita pochitira zamatsenga m’busayo ndi cholinga chomuopyeza kuti achoke.


Apindilana ndevu mkamwa kamba kolimbilana mkazi
Amuna awiri apa mudzi wa Mpunga kwa Kapeni ku Chigumula m’boma la Blantyre anagwira pakhosi mpaka kupindirana ndevu mkamwa polimbirana mkazi wachibwenzi. Nkhaniyi ikuti amuna awiriwo anali pa ubwenzi wa nseri ndi mkazi m’modzi koma samadziwana. Tsiku lina m’modzi mwa amunawo yemwenso ndi wa geni anagulira mkazi wachibwenziyo katundu wa golosale. Apa mwamunayo pamodzi ndi mkazi wachibwenziyo amayenda pamodzi uku mwamunayo akutsatsa malonda ake pomwe mwadzidzidzi anakomana ndi mwamuna m’nzakeyo. Apa mwamuna winayo anangofikira kusama pakhosi mwamuna m’nzakeyo ponena kuti bwanji akuyenda monyada ndi bwenzi lake? Apo panali ndeu ya mtima bii kotero kuti anthu ena ndiwo analeletsa nkhondoyo. Koma pa nthawiyo nkuti mwamuna yemwe anayamba kusama m’nzakeyo pakhosi magazi akuthoboka mphuno ndi mkamwa ngati akutuluka pa mpope. Pakadalipano mwamuna wa malondayo wachenjeza m’nzakeyo kuti adzamuonetsa chomwe chidameta nkhanga mpala akadzayerekezanso kuchingira kuti asayende ndi mkazi wachibwenziyo.

Get Your Newsletter