Nkhaniyi ikuti mnyamatayo anapita ku mowa ndipo pobwera anali dzandi-dzandi chifukwa cha bibida yemwe anamwa. Atafika pakhomopo anapeza mai ake akuchokela ku munda ndipo anawalalatila uku akunena kuti amupatse msima chifukwa anali ndi njala. Mai akewo anamupatsa msima koma ndiwo zinali zochepa. Pamenepa mkangano unakula mpaka mnyamatayo anagwira mai akewo ndikuwamenya ndi mpini wakhasu. Chifukwa choti maiwo anavulala kwambiri m’mutu anagwa pansi nkukomoka. Mnyamatayo ataona izi anathawa mpaka sanabwerele ku nyumbako. Anthu ambiri adandaula ndi khalidwe la mnyamatayo lowachitila nkhaza mai ake chikhalilecho bamboo ake anamwalira koma amamusamala ndi mai akewo. Pakadali pano anthu ena akufunafuna mnyamatayo ndipo ati akamupeza amukokela kwa akulu-akulu azachitetezo mderalo.
Banja lina likhala mwamantha
Banja lina ku Chigumula mu mzinda wa Blantyre likukhala mwa mantha chifukwa cha mkangano omwe ulipo pakati pawo ndi banja lina loyandikana nalo nyumba. Nkhaniyi ikuti banjali linagula nyumba ndi malo olima koma malowo ndi omwe banja linalo lakhalanso likuwafuna kuyambira kale koma limalephera kugula malinga m;mavuto azachuma. Pachifukwachi eni mundawo akamagwira ntchito zao zakumunda, banja linalo limangokhalila kulalata pa zifukwa zosadziwika. Atatopa ndi khalidweli banjalo linatengera nkhaniyi kwa Nyakwawa ndipo inayitana anthu onsewo kuti akakomane ku munda-ko. Chodabwitsa ndi choti atangofika pa mundapo , mwini mundawo anagwa pansi nkukomoka. Nthawi yomweyo mfumuyo inanyanyala nkuchoka pa malopo. Koma maiyo atadzidzimuka banja linalo linapitiliza kuchitila chipongwe mayiyo zomwe zinadabwitsa anthu omwe amayang’anila munthu okomokayo. Pakadali pano anthu ambiri adzudzula zamatsenga zomwe zinachitika kumundako komabe eni mundawo anenetsa kuti zivute zitani sasiya kulima mundawo.