Nkhaniyi ikuti Mbusayo amakhala mudzi umodzi ndi mchimwene wakeyo ndipo akuti anthuwa amagwirizana kwambiri posadziwa kuti mbusayo anadyelera maso mkazi wa mbale wake. Pa tsikulo mbusayo anafika pakhomo pa mchimwene wakeyo ndipo anapeza mbale wakeyo kulibe. Apa anangoti laponda la mphawi diwa ndipo anamukokera mlamu wakeyo ku chipinda koma mwatsoka anawapezelera. Nkhaniyi yafala m’mudzi onsewo zomwe zachititsa kuti akhrsitu a mpingo wa mbusayo ataye chikhulipiliro mwa iye. Pakadali pano nkhaniyi yakafika ku bwalo ndipo kuyambira pa tsikulo mbusayo akuyenda mozemba pochita manyazi ndi nkhaniyi.
Abisala kuphiri kamba kothawa mlandu
Mkulu wina kwa Mazengera m’boma la Lilongwe wathawa ndipo akubisala ku phiri powopa mlandu ogwilira mtsikana ozelezeka. Nkhaniyi ikuti mkuluyu ali pa banja ndipo anabeleka ana angapo. Pa zifukwa zosadziwika mkuluyu anagwirila mtsikana odzeredzeka. Nkhaniyi itadziwika anthu m’mudzimo anakamang’ala kwa nyakwawa komwe sanachedwe koma kuitanitsa mkuluyu kuti akayankhe mlandu. M’malo mopita kwa nyakwawayo Mkuuyo akuti anangoliyatsa liwiro waku phiri komwe akubisala. Kenaka nyakwawayo idalamula anthu kuti apite ku phiriko kukamusaka-saka koma sadampeze. Pakadali pano anthu akudikirabe mkuluyo kuti akadzabwera ku phiri-ko akayakhe mlandu .