09/05/15

Written by  Newsroom

Akhumudwa atawona nkhope ya chibwenzi chapa facebook
Mkulu wina yemwe amakhala ku Lilongwe wabwelera manja ali m’khosi pa ulendo wake omwe anapita ku Blantyre kukaonana ndi chibwenzi chake chomwe anachipeza pa FACEBOOK.

11
May

Nkhaniyi ikuti mkuluyo wakhala akulumikizana ndi mtsikana wina pa Facebook mpaka kufunsirana chibwenzi. Chibwenzicho chitafumbira mkuluyo anaganiza zokaonana maso ndi maso ndi mtsikanayo ndipo anapita dzulo kwa Lundu komwe kumakhala mtsikanayo. Mtsikanayo atamuona mkuluyo anaonetsa nkhope yakugwa ati kamba koti nkhope ya mkuluyo imasiyana kwambiri ndi momwe imaonekera pa FACEBOOK-PO. Mwa zina mkuluyo akuti ndi wamkulu kwambiri poyerekeza ndi zaka 16 za mtsikanayo yemwe akuti ali MU Form 2 pa sukulu ina ya sekondale m’deralo. Mkuluyo akuti wachoka atakhumudwa kwambiri mtsikanayo atamulandula kuti chibwenzicho chatha. Anthu ena omwe amva nkhaniyi ati nkutheka kuti mtsikanayo walimba mtima ndi chibwenzi chomwe wachita ndi mnyamata wina yemwe wabwera kuchokera ku Joni posachedwapa.

 

Nkangano ubuka polimbilana munda
Mwamuna wina kwa Ntchema m’boma la Chiradzulu walolera kusiya munda wake pofuna kupulumutsa moyo pa mkangano wolimbirana munda ndi mbale wake. Nkhaniyi ikuti amuna awiri apa chibale m’mudzimo akuonana ndi diso la nkhwezule chifukwa chokanganilana dimba lomwe anasiya makolo ao. Makolowo atamwalira anasiya munda komanso dimba zomwe anayamba kukanganilana. Pa mkanganowo m’modzi mwa iwo amafuna kuti azilima yekha mundawo komanso dimbalo. Polephera kumvana bwino anatengera nkhaniyi kwa nyakwawa koma palibe chomwe anaphula chifukwa amuna awiriwo samagwirizana pa nkhaniyi. Pa chifukwachi anthu anangowasiya kuti athane okha. Ndipo tsiku lina m’modzi mwa amunawo anatenga khasu ndikukayamba kulima kumundako koma winayo atamva izi , anatenga chikwanje ndikuyamba kuthamangisa nzakeyo kuzunguilira mundawo. M‘bale wakeyo ataona kuti zavuta anangosiya khasu nkuthawa ndipo mpaka pano sanabwelerenso pa khomo. Pakadali pano anthu ena adzudzula zomwe amuna awiriwo akuchita ponena kuti nzachilendo m’mudzimo.

Get Your Newsletter