08/05/15

Written by  Newsroom

Mafumu awiri akunthana pamaliro
Mwambo wa Maliro unasokonezeka mdera la mfumu Mwasambo m’boma la Karonga mafumu awiri atakhuthana koopsya polimbilana kulankhula pa mwambowo.

11
May

Nkhani-yi ikuti mderalo kunachitika maliro ndipo a mpingo anayendetsa bwino mwambowo. Kenako ampingowo anapeleka mwai kuti mafumu alankhule popitiliza mwambowo. Koma chifukwa choti pa malopo panali mafumu awiri , Mfumu yaikulu inadzuka mkuyamba kulakhula yaing’ono isanalankhule. Powona kuti mfumu yaing’ono inalibe mwai woti ilankhule mfumu yaikulu italankhula kale , inajejemetsa mfumu yaikuluyo kuti ikhale pansi kuti mfumu yaing’onoyo ilakhule. Posavana bwino pa nkhaniyi mafumuwo anayamba kukangana mpaka kuponyerana zigogodo mpaka kuyamba kugudubuzana ndikugwetsana mufumbi. Anthu omwe anasongana pa maliropo anayamba kuleletsa ndewuyo . Pamenepa mfumu yaikuluyo inapeza mpata ndikuchoka pa malopo ndikuliyatsa liwiro la mtondo wadooka . Izi zinakhumudwitsa a mpingo omwe amayendetsa malirowo. Zikumveka kuti mfumu yaikuluyo inavulala kwambiri pa ndewuyo.

 

 

Anyamata awiri achita ubwenzi ndi mkazi m'modzi 
Mtsikana wina kwa Kanduku mboma la Mwanza akuyenda cheu-cheu anyamata ena awiri omwe anali nawo pa chibwenzi atamupanganira kuti amukuntha ngati sawabwezera zawo. Nkhaniyi ikuti poyamba mtsikanayo anachita chibwenzi ndi m’modzi mwa anyamatawo ndipo kenaka analolanso winayo koma chikhalirecho ali nd mwamuna wina yemwe anagwirizana naye za banja koma anapita kukagwira ntchito ku Mozambique. Tsono chavumbulutsa mavu pa chisa nchakuti m’modzi mwa anyamatawo anatenga phone ya mkaziyo ndipo kenaka anadzayimba phone ina yomwe imaonetsa kuti mkaziyo anayiyimba posakhalitsa koma anadabwa kuti anayankha phoneyo anali munthu wa mwamuna. Apa mnyamatayo sanamufunse koma m’malo mwake anangotenga nambala ya phoneyo nkuyamba kufufuza mwini nambalayo. Atamupeza anamufunsa za mkaziyo ndipo anavomera kuti ndi bwenzi lake. Apa anyamatawo anangogwirizana kuti athetse chibwenzi ndi mtsikanayo ndikumulamula kuti awabwezere zinthu zonse zomwe akhala kumupatsa. Anyamatawo achenjeza kuti ngati sabweza zinthuzo amukuntha. Pakadali pano mtsikanayo akuyenda mwa mantha ndipo sizikudziwika kuti mwamuna waku Mozambique-yo akadzamva nkhaniyi sidzatha bwanji. Koma anthu omwe akumudziwa bwino mtsikanayo ati ndi khalidwe lake la chimasomaso chifukwa m’mbuyomu anyamata ena anakunthananso mpaka kukhapana chifukwa choimbirana mtsikanayo.

Get Your Newsletter