06/05/15

Written by  Newsroom

Agwa padenga posasula Malata kamba ka Nsanje
Mai wina kwa Mwadyawathu m’boma la Kasungu ali mu ulu woopsya atagwa pa denga la nyumba ndikuvulala pamene amasasula Malata chifukwa cha Nsanje.

06
May

Nkhaniyi ikuti mai-yo anakwatiwa ndi mwamuna wina ndikubelekera ana asanu ndi awiri. Ndipo tsiku lina maiyo anapita kwao kokolola ndipo m’buyomu mwamuna wake anagwa mchikondi ndi mkazi wina yemwe amachita malonda ogulitsa thobwa pa msika wina mderalo. Chibwenzicho chitafunga anthu awiriwo anagwirizana zoti akwatilane. Kenako onse anatengana kukaonekera kwa makolo ake a mai-yo. Koma Mkazi mwini mwamunayo atamaliza ntchito yonse yomwe anakagwira kumudzi anabwerela kwao koma anapeza pakhomopo pali pulululu. Anthu oyandikana ndi nyumbayo analuma khutu mkaziyo kuti mwamunayo anatengana ndi mkazi wina ndipo anapita kwao. Pamenepa mkazi-yo anayimbila telefoni mwamunayo kuti afotokoze komwe anali koma iye sanazengereze koma kumuuza mkaziyo kuti tsopano wapeza mkazi wina wachiwiri. Chifukwa chopsya mtima mkaziyo anakwera pa denga la nyumbayo mkuyamba kusasula Malata ndi cholinga choti atenge malatawo ndikusiya pa nkhomopo palibe chili chonse. Koma ali pa dengapo maiyo anatsakamuka kugwa pansi ndikuthyola nkono. Pakadali pano maiyo sakupeza bwino.

 

 

Anama za maliro wa munthu wakundende
Mafumu ndi mikoko yogona pamudzi wina ku Pengapenga kwa mfumu Mwakwangwara m’boma la Ntcheu athedwa nzeru malingana ndi zomwe munthu wina adanamiza anthu pamudzipo kuti m’bale wawo yemwe ali ku ndende wamwalira. Nkhaniyi ikuti munthu wina pamudzipo adapalamula mlandu ndipo a khothi adamulamula kuti akakhale ku ndende zaka zisanu. Ali kundendeko munthu wina yemwe ndi mthira kuwiri anakauza aku banja kuti m’bale wawo wamwalira ku ndendeko. Monga mwa mwambo wake anthu aku banja anaitanitsa gule wamkulu yemwe anachezera kuvina pa Siwapo . Koma m’mawa kutacha a ku banja anadzidzimuka atalandila uthenga kuchokera ku ndende kuti m’bale wawo-yo akadali moyo. Munthu yemwe anabweretsa uthenga uja tazindikira kuti nkhaniyi yawanda kuti munthuyo sanamwalire mkuluyo wathawa pa mudzipo ndipo sakudziwika komwe walowera. Izi zaimitsa mitu mikoko yogona kuti cholinga cha munthu ameneyu chinali chani.

Get Your Newsletter