Nkhaniyi ikuti bamboyo wakhala akuzembera anawo omwe ndi a zaka zisanu ndi zitatu ndi khumi powaopyezsa kuti akadzaulura adzachoka pakhomopo pamodzi ndi mayi awo. Tsiku lina mayiyo anadzidzimuka ndipo amafuna kuti akataye madzi, koma anangoona kuti bamboyo palibe pa mphasapo. Atayitana bamboyo sanavomere ndipo mayiyo anangoganiza zopita ku chipinda cha anawo ndipo bamboyo anadzambatuka ndikunena kuti amafuna kuti akaone momwe anawo amagonera ngati njira imodzi yowayang’anila. Apa anawo ndi pamene anauula za nkhaniyo kwa mayi awo ndipo banja linathera pomwepo. Anthu mderalo akudzudzula kwambiri bamboyo ndipo pakadali pano asowa m’mudzimo.
Kanyama kachilendo kazizitswa mayi wina
Mai wa m’mudzi wina mdera la mfumu Kalonga ku Salima anadzidzimuka pamene adakumana ndikanyama kena kali ndi mazingano thupi lonse komwe kanayima pakati pamphambano. Nkhaniyi ikuti pasiku apitawa mayiyu adalawira kum’mawa kupita ndicholinga chopita kumunda kukakumba mtedza. koma atafika pamphano yopita kumunda kwake adaona kanyama kena kofanana ndi mpahaka katayima njira yomwe iye amati adutse. malingana pakuti kudali kusadayere mayiyu amaganiza kuti mwina ndi bvumbwe. koma pamene adayandikira adadzidzimuka pamenme adaona kuti mphakayo adali ndizingano nthupi lake lonse. Apa mayiyu sadapitilize ulendo wake adabwerera kumudzi kukauza mikoko yogona zamalodzawo.mosankhalaitsa mikoko yogonayo itamva zankhaniyi sidachedwe koma kulunjika kumaloko. atafika pamalopo adapeza kuti mphaka wodatsiya adagokala du osasuthika. koma pamene adatenga chida kuti amukanthe apa mphaka adazida thungozo mpaka kenaka adazimilira osamuonanso.