Nkhaniyi ikuti mayiyo amayang’anila odwala pa chipatala china mderalo, koma chodabwitsa nchakuti anapezeleredwa akuchita zachisembwere pa malo ena olandila alendo nkusiya odwala ali yekha yekha mchipinda chodwazika odwala. Mamuna wina yemwe anakhalapo nduna ya Mfumuyo ndi amene anaona mayiyo akucheza ndi doda wina mpaka kukalowa naye mchipinda china , Mkuluyo amaonetsetsa mwa chidwi pamene mayiyo samamuona mkuluyo. Apo mkuluyo pokhala kuti anamuchotsa pa udindo chifukwa cha mabodza a amyiyo nayenso anangoti ndi mwayi wake kuti akafotokozere mfumuyo. Mwachangu mfumuyo inafika pa malopo ndikulamulira apa malopo kuti amutulutsile omwe anali mchipindacho, koma ngakhale analimbabe kumapeto kwake anatulutsa anthuwo. Mayiyo ataona a mfumuwo anadzigwetsa pansi kupepesa koma Mfumuyo inauza mayiyo pomwepo kuti banja latha.
Achita zachisembwere kuchipatala magetsi atazima
Anthu mchipinda cha odwala mdera la Kagulo m’boma la Zomba ndiwokhumudwa kwambiri ndi zomwe anachita m’modzi mwa odwala pa chipatalacho kuchita za chisembwere ndi mkazi wake pamene magetsi apa malopo atazima usiku. Izi zinadziwika pamene magetsiwo anayaka mwadzidzi ndipo anthuwo anaona ngati kutulo kuona kuti bamboyo akudzambatuka pa bedipo. Anthu pa chipatalacho komanso deralo adzudzula kwambiri bamboyo ati malo moti aganizile za kudwala kwake nkukhala ndi maganizo opusa ngati amenewa.