Nkhaniyi ikuti mwamuna wa mayiyo amagwira ntchito pa chigayo ndipo mayiyo amakhalira kumunyoza mwamuna wakeyo ati chifukwa choti nthawi zambiri amakhala ali m’maluzi. Izi zakhala zikukhumudwitsa mwamunayo ndipo akamudzudzula mkazi amayankha mokhadzula kuti iye akutuwa chifukwa choti mwamuna-yo ndi kapuntha buye. Mkaziyo akuti mwa zina anasiya kugwira ntchito zapa khomo ncholinga choti mwamunayo akwiye ndikuchoka pakhomopo ndipo anachokadi kubwelera kwao. Mphuno salota mwamuna yemwe amamunamiza mkaziyo kuti amukwatira ndi Dobadoba ndipo anasintha poyerayera ndikunena kuti samukwatiranso mkaziyo. Anthu mderalo akumuseka mayiyo chifukwa chopasula banja lake ndi manja ake ndipo pakadali pano ndi mbeta.
Ntchito itha kamba kochedwa
Mkulu wina yemwe amagwira ntchito yaulonda ku Sangazi mu mzinda wa Mzuzu akulira usana ndi usiku ntchito yake itatha dzuwa likuswa mtengo chifukwa chochedwa ku ntchito pa zifukwa zosadziwika bwino. Mabwana apa ntchitopo akuti akhala akumudzudzula mkuluyo chifukwa cha khalidwe lakelo koma m’malo mokhuzumuka akuti amabweza moto kwa mabwanawo. Pa tsikulo, mkuluyo akuti anachedwa kwambiri ndipo bwana ake pomudzudzula anayamba kukangana nao mpaka ndeu ya fumbi kobo kubuka pakati pa anthu awiriwo. Pa ndeuyo, mlondayo akuti amachepera kaba mpaka anaguluka mano. Tsono ataona kuti zavuta mkuluyo akuti anayamba kupepesa kwa bwanayo Bwanayo sanaimve mpaka pomaliza anamuuza kuti ntchito yake yatha pompopompo. Apa mkuluyo akuti analira kwachitika maliro ati ncholinga choti Bwanayo amukhulukire koma sizinatheke. Pakadali pano, mkuluyo akulira usana ndi usiku kulilira ntchitoyo ponena kuti saipezanso ina.