Nkhani-yi ikuti mbusa-yo wakhala kugwila ntchito ndi mlembi wake-yo popanda vuto koma kenaka mbusa-yo anayamba kudyelela maso mwamuna-yo mpaka kumufinsila. Koma mwamuna-yo wakhala kukana kukhala pa ubwenzi ndi mbusa-yo. Tsiku lina mbusa-yo akuti anatopa kufunsila mwa ulemu mlembi-yo ndipo anaganiza njira ina yothanilana ndi mwamuna-yo. Awiri-wo akugwila ntchito zina ku ofesi ya mpingo-wo mbusa-yo akuti anayamba kufuna zogonana ndi mwamuna wa mwini-yo pomwe anayamba kumugwila malo osayenela. Mwamuna-yo ataona kuti zinthu ziipa akuti anathawa-wa. Mai-yo akuti sanasiile pomwe-po koma kuthamangila mkulu-yo yemwe anaganiza mwa changu mkuthawila ku manda ena mdera-lo.
Mpunzitsi aba thumba la nyemba
Anthu okhala pafupi ndi sitolo zapa Bangula m’boma la Nsanje ati ndiokhumudwa ndizomwe wachita mphunzitsi wina wapa sukulu ina ya sekondale yogonera komweko mderalo poba thumba la nyemba zapa sukulupo. Nkhaniyi ikuti mphunzitsiyo akhala akumukaikira kuti ndi m’modzi mwa mbava zomwe zakhala zikuba zakudya za ana apa sukulupo chifukwa cha mayendedwe ake. Pa tsikulo, mphunzitsiyo akuti anagwirizana ndi m’modzi mwa ophunzila apa sukulupo kuti amunyamulire thumba la nyemba popeza aphunzitsi ena anachoka. Mwa tsoka, ophunzira yemwe ananyamula thumba la nyembalo pa njinga yakapalasa anangoti gululu ndi ophunzira ena omwe anampanikiza mpaka kukabweza thumbalo. Pakadali pano, nkhaniyi ili m’manja mwa sukulu komiti komanso mphunzitsi wamkulu wapa sukulupo ndipo mphunzitsi wakubayo akubindikira mnyumba chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi. Anthu ambiri mderalo ati ndiokhummudwa ndizomwe wachita mphunzitsiyo malinga nkuti anayenera kuonetsa chitsanzo chabwino.