Nkhaniyi ikuti mayiyo tsiku lina anapita pa mjigopo pomwe anapeza anthu ochuluka ali pa mzere kufuna kutunga madzi, ndipo mwa khalidwe lake anapitilira anthuwo ndikupita patsogolo. Anthu ena pomufunsa mayiyo chifukwa chomwe amachitila izi anayamba kuwalalatila kwinaku akunena mwathamo kuti iye ngochokera ku banja lodziwika bwino m’mudzimo. Paja amati ya fote ikakwana, atsikana ena omwe anali pa mjigopo sanaimve ndipo anagwirizana zothidzimula mayiyo mpaka anachoka chothamanga pa malopo uku akukuwa ku NDITHANDIZENI CHONDE koma palibe munthu ndi m’modzi yemwe anamuvera chisoni. Anthu omwe anali pa mjigopo anayamikira atsikanawo ponena kuti agwira ntchito yotamandika. Pakadali pano mayi wodziwikayo wadula phazi pa mjigopo ndipo akumatunga madzi ku dera lina lapatali ndi pamalopo.
Anthu akhumudwa ndi zochitika za mkulu wina
Mwamuna wina wa mudzi wa Kamchepela mdera la Chinyama yemwe amagwira ntchito pa farm ina m’boma la Kasungu wakhumudwitsa anthu m’deralo chifukwa cha khalidwe lake lomwa mowa mwauchidakwa. Nkhaniyi ikuti bamboyo yemwe ndi m’modzi mwa anthu odalilika pa farmyo anapita kukamwa mowa mpakana kulephera kuyenda ndikugona panjira. Anthu ena akufuna kwabwino ataona bamboyo anakafotokozera bwana wakeyo za nkhaniyi. Bwanayo atalandila uthengawo sanazengereze mpaka anakauza wangolo kuti amutenge bamboyo. Koma chinaseketsa anthu a m’mudzimo mchakuti eni ngolowo ananenetsa kuti ayambe kaye kuwalipila asananyamule bamboyo ati ponena kuti sanali mavuto ogwa mwadzidzi koma zofuna dala choncho anakanitsitsa ngongole. Bwana wa mkuluyo anapereka ndalama yokwana 2-thousand five hundred kwacha. Pakadali pano mkuluyo akukhala mobindikira chifukwa cha manyazi.