26/04/15

Written by  Newsroom

Alira ngati maliro mkazi atathesa ukwati
Mnyamata wina ku Chipoka m’boma la Salima wadabwitsa mikoko yogona atalira mokweza ati kamba koti mkazi wake wamusiya ukwati ati chifukwa choti mnyamatayo anaba chimanga cha apongozi ake.

27
April

Nkhaniyi ikuti mnyamatayo wakhala akutchuka ndi mbiri yoba chimanga komanso Mbatata minda komanso Mmadimba. Mkazi wakeyo wakhala akumva zonsezi ndipo amamufunsa mwamuna wakeyo ndipo wakhala akumudzudzula kuti asiye khalidwe lonyasalo. Koma tsikuli mnyamatayo anapita kwa apongozi ake koma tsoka ilo apongozi akewo sanawapeze zomwe zinapangitsa kuti apezerepo mwayi wothyola nyumba ya apongozi akewo ndikuba thumba la chimanga. Mkazi wamnyamatayo atamva izi anakwiya kwambiri ndipo analongedza katundu wake ndikuchoka pa khomo pa mnyamatayo. Pakadali pano mkaziyo wamenyetsa nkhangwa pa mwala kuti sangabwerenso kunyumba kwa mnyamatayo ati kamba koti watopa ndi mkhalidwe la mnyamatayo lomwe wati lafika posauzana.


Mwana wa sukulu akunthidwa kamba kochita ubwenzi ndi mphunzitsi
Mtsikana wina wapa sukulu ina kwa Kachere m’boma la Dedza amuswa kodetsa nkhawa mkazi wa mwamuna wa mphunzitsi wina yemwe anali naye pa chibwezi atamupezelela ali mchikondi ndi mwamuna wakeyo. Nkhaniyi ikuti mphunzitsi wina wap asukulu ina mderalo masiku apitawa anagwa mchikondi ndi mtsika wapa sukulupo mpaka chibwenzi chao chinafumbila. Kwanthawi yaitali mkuluyo amati akamaliza kumphunzitsa amamunyengerela mtsikanayo kuti apite ku malo ogona alendo. Tsiku lina mwamunayo atamuuza mkazi wake kuti akukagula soap ku sitolozo , mkazi wake anaganiza zotsatila kumsika anthu ena atamutsinanso khutu kuti mkuluyo wapangila akumalowa ku malo ogona alendo ndi mtsikanayo. Mkaziyo akuti anazizila nkhokhono atapeza awiliwo ali mchikondi dzuwa likuswa mtengo. Pamenepa akuti panabuka ndeu yosowa oleletsa mpaka mwana wa sukuluyo nkhope yake kutupa ngati chitumbuwa. Panopa, anthu ambili akudzudzula makolo a mtsikanayo wakubayo pomulekelela kumachita zachisembwele ndi amuna osiyana siyana ati ncholinga choti azidya zankhuli zomwe zikuika moyo wake pa chiswe.

Get Your Newsletter