Nkhaniyi ikuti apa mudzi wina akhumudwa kwambiri chifukwa chakusagwirizana komwe kwabuka pakati pa anthu ambali ziwrizi omwe akulimbilana ufumu koma sakugonjelana wina ndi nzake. Kenako mfumu yaikulu ya m’mudzimo inayitanitsa mabanja onse onkhuzidwa koma mfumuyo isanayambe kulankhula anthuwo anayamba kunyogodolana mpaka kumutema yemwe akuyembekezeka kulowa ufumuwo. Pamenepa ndeu yosowa oleletsa inabuka . Zikumveka kuti anthu ena mpaka anaba mipando ya pa bwalo pa mfumuwo. Kenako achitetezo a m’mudzimo akuti ndi amene anathandiza kuti ndewuyo isapitilire. Pakadali pano mfumu yaikuluyo yalamula anthu omwe anayambitsa ndewuyo kuti apeleke mbudzi ziwiri aliyense chifukwa chonyatsisa bwalo la mfumu. Panopa,anthu akumeneko akuti akuonana ndi diso lofiila chifukwa cha nkhani-yo ndipo anthu ambili akudzudzula anthuwo akubweretsa khalidwe loiyipa m’mudzimo.
Chisokonezo pamaliro
Mwambo wa maliro unasokonezeka kwa Mfumu Ganya m’boma la Ntcheu a mpingo atawaletsa mafumu kuchita mwambo wachifumu pa malirowo. Nkhaniyi ikuti m’mudzimo munagwa zovuta pamene mfumu ina inamwalira mwadzidzidzi. Chifukwa choti mfumuyo inali yopemphera kwambiri ampingo anayamba kuyimba nyimbo za maliro ndipo anachezera pa siwapo. Koma chifukwa choti mfumu ikamwalira pamayenera kuchitika mwambo wapadera omwe mafumu amachita , izi zinasokonekera chifukwa choti m’busa wa mpingowo analamula kuti mafumuwo asatenge mbali ina iliyonse pa malirowo. Pamenepa mfumu yaikulu ndi nyakwa zina zinakwiya kwambiri ndipo anayamba kubalalika pa maliro. Koma eni mbumba anachondelera mafumuwo ndipo potengera chikhalidwe cha mfumu yomwe inamwalilayo mafumuwo anakhululuka mkukhala nao pa maliropo koma sanalankhule . Pamene chifukwa chokwiya a mpingowo anangoyendesa mwambowo mwachidule moti panalibenso mwambo wakhata, Pakadali pano anthu a ‘mudzimo akulozaloza chala m’busa wa mpingowo chifukwa chosalemekeza mafumu.