Nkhaniyi ikuti tsiku lina amai awiriwa anapita kumapemphero a usiku limodzi koma m’modzi wa maiyo anasanzika nzake kuti watopa ndipo akukagona panja pa tchalichicho ndipo mzakeyo anavomera. Koma m’malo mogona panjapo maiyo anazemba ndikupita kwa mwamuna wa nzakeyo yemwe anali naye pa chibwanzi cha nseli kwa nthawi yaitali.Koma mai uja mwini mwamunayo atatuluka mchalichimo sanamupeze nzakeyo. Koma kutacha maiyo atapita ku nyumba kwake sanakapeze mwamuna wake. Mwamunayo anabwera ku nyumbako masana ndipo atamuphaphalisa ndi mafunso anangoti ndwiii. nthawi yomwe maiyo anamuikila madzi kubafa kuti mwamunayo akasambe ndipo ali kosambako pa foni yake ya m’manja panabwera uthenga omwe umakamba zabwino zonse zomwe anachita usiku. Maiyo ataona nambala yomwe inali pa foniyo anadzidzimuka poona kuti idali ya mai uja amacheza naye kwambiri. Nthawi yomweyo sanachedwe koma kulunjika kunyumba kwacha kwa nzakeyo. Zinthu zinavuta ndipo chindeu choopsya chinabuka mpaka kung’ambirana zovala. Mai wakubayo analiyatsa liwiro kuthawira kuseri kwa sitolo za pa malopo. Nkhaniyi itafikwa kwa akuluakulu ampingo anakhumudwa ndipo awayimitsa kaye mu mpingo. Pakadali pano ukwatiwo wagwedezeka kwambiri.
Ataya khanda nchimbudzi
Anthu omwe anali mu khothi lina ku Ulongwe mboma la Balaka anagwetsa ulesi anthu omwe anamvera mlandu atapempha khothi kuti limukhululukile kamba kotaya khanda mchimbudzi. Nkhani-yi ikuti mai-yo ali ndi ana kale asanu ndi awiri ndipo oyamba wake ali ndi zaka khumi ndi ziwiri pamene wangono ali ndi chaka chimodzi. Masiku ochepa apita-wa mai-yo akuti anabereka mwana wa mwamuna ndipo anataya khanda-lo mchimbu-zi opanda anthu kudziwa kuti mai-yo wachila. Koma anthu ena atadabwa kuti mai-yo sakuoneka oyembekezela anauza apolisi pokaikika kuti mai-yo wapha khanda-lo. Apa mai-yo anavomera kuti anabeleka mwana-yo ndipo anamuponya mchimbudzi. Koma anthu atagumula chimbudzi-cho anapeza khanda-lo litafa kale. Popela chidandaulo mai-yo anapempha khothi-lo kuti limukhululukile kamba koti ndi osauka ndipo ali ndi chi udindo chachikulu. Iye anati amasamalila amai ake omwe ndi okalamba, ana ake asanu ndi awiri ndipo sali pa banja. Mai-yo anauza khothi-lo kuti anataya mwana-yo chifukwa choti mwamuna yemwe anamupatsa pakati anamukana ndipo anathawa mdera-lo. Ndipo popereka chigamulo a magistrate analamula mai-yo kuti agwile ukaidi wakunja posesa pa sukulu ya pulaimale ya Nkhonde kwa miezi isanu. Magistrate-yo anati anapereka chilango cha ukadi wakunja kuti mai-yo asamale ana ake-wo.