23/04/15

Written by  Newsroom

Mbusa amenyana ndi mlembi kamba ka malo
M’busa wa mpingo wina ku Tsangano m’boma la Ntcheu akuti wamenyana koopsya ndi mlembi wake wa mpingowu chifukwa chokanganila malo.

27
April

Nkhaniyi ikuti m’busayo wangofika kumene ndipo akuluakulu ampingo atamulandila pa malopo anamupasa munda. Koma chifukwa choti malowo anali ochepa m’busayo anayitanitsa mnsokhano wa akulu akulu okha-okha a mu mpingowo ndi kunenetsa kuti iye salola kukhala ndi malo ochepa pamene mlembi ali ndi malo akulu. Pamenepa kusamvana kunabuka ndipo palibe chogwira mtima chimene anagwirizana pa mnsokhanopo . Tsono kutacha m’busayo anatuma a ntchito ake ndikagumula mgula umene unachita malire ndi mlembiyo . Kenaka akuluakulu antchitowo anazala kholowa . Izi sizinakomele mlembiyo yemwe anapita ku mpanda kwa m;busako ndikuyamba kulalata. Koma M’busayo anamasula agalu ake ndikuyamba kutamangitsa mlembiyo osadziwa kuti anali ndi chibonga chomwe anaponyela m’busayo ndikugwa pansi . Anthu ambiri analowerela poleletsa ndewuyo koma m’busayo atavulala. A komiti ya mpingowo anatengela m’busayo ku chipatala china mderalo koma a akuti sakupeza bwino.

 

Aletsa mwambo oveka nyakwawa
Anthu wokhala pamudzi wina mdera la Kawinga mboma la Machinga anazizila nkhongono komanso kulila ngati kwagwa malilo ndi zomwe mkulu wina anachita poletsa mwambo wobveka unyakwawa namwali ali panja kuti anthu ayambe kufupa komanso kumuveka nduwila.Nkhani-yi ikuti mderalo kuli anthu awili omwe akulimbilana unyakwawa koma anthu m’mudzimo amafuna kwambili wam’ngono chifukwa chakhalidwe lake lodzichepetsa mpaka anthu anamugwila kuti ndiye akhale nyakwawa. Zokonzekela zones zamwambowo zinayenda bwino mpaka kupha mbudzi zinai komanso kuitana anthu ndi abale ochokera m’madera osiyanasiyana . Anthu akuti anachezela bwino lomwe usiku povina chindimba kuti tsopano kukacha akhala ndi nyakwawa yatsopano. Koma kutacha m’mawa akulu akulu osiyana siyana atafika kale kudzaveka ufumu-wo anthu ali pa bwalo anadabwa kuona munthu wina akufika ndi chikalata choletsa mwambo-wo kuti sutheka kamba koti bwalo lamilandu laletsa. Zimenezi akuti zinadzetsa mfuwu ngati pagwa zovuta kotero kuti anthu ngakhale amakhwasula nyama kuphwanya mafuta komabe sanali wokondwa podziwa kuti palibe chomwe anachita. Panopa, anthu akumeneko akuti akuonana ndi diso lofiila chifukwa cha nkhani-yo ndipo anthu ambili akudzudzula wamkulu-yo kuti ndiye wosokoneza ndikuti ufumu sadzaununkha mtsogolo.

Get Your Newsletter