22/04/15

Written by  Newsroom

Atumizilidwa njoka kamba koyenda ndi mayi wapabanja
Mnyamata wina ogulitsa nyama ya mbudzi pa msika wina kwa mfumu Mtwalo mboma la Mzimba wathawa pa malo pake pa bizinesi mwamuna wa mkazi yemwe anali naye pa chibwenzi atatumiza njoka ya masenga kuti ithane ndi mkuluyo pa malopo.

27
April

Nkhaniyi ikuti mwamuna wa bisinesi-yo anapalana ubwenzi wa nseli ndi mai wina yemwe mwamuna wake amagwira ntchito yolambula mseu m’boma la Chitipa. Mwamuna wa mkaziyo wakhala akudabwa kuti akapeleka ndalama yochepa , mkazi wakeyo amagulabe nyama ngakhale zitavuta motani. Tsiku lina anthu anadabwa kuona mkaziyo akulowa pa Butchery ina mozemba ndipo nthawi yomweyo mkaziyo anapasidwa chakumwa chozizilitsa kukhosi ndi tchipisi. Kenako anthu ena anakaluma khutu mwini mwamunayo. Maiyo atafika kunyumbako mwamunayo anamuphaphalitsa ndi mafunso omwe mai-yo anachita chibwibwi poyankha. Mwamunayo anakafotokozera nkhaniyi malume ake. Koma amalumewo anamubweza mnzukulu wakeyo ndikumutsimikiza kuti achita zodabwitsa mpaka mwamuna wakubayo athawa yekha. Posakhalitsa anthu anava kukuwa pa malo ogulisira nyamayo. Anthu atathamangira pa malopo anadabwa kuona njoka yayikulu ikulimbana ndi mkuluyo. Chifukwa cha mantha mkuluyo analiyatsa liwiro kuthawa pa malo ake-wo ndipo mpaka pano sakuwoneka,


Akomola mnyamata wina kamba ka Nsanje
Anthu ena ku Namwera kwa mfumu Jasalasi m’boma la Jalasi ati akhumudwa kwambiri ndizomwe achita anyamata ena pomenya mwamuna wina mpaka kumukomola chifukwa cha nsanje. Nkhaniyi ikuti mai wina anakwatiwa ndi njonda ina yomwe imagulitsa zovala mderalo. Koma pa zifukwa zina ukwatiwo unatha. Mkaziyo wakhala zaka ziwiri asali pa banja ndipo tsiku lina anagwa mchikondi ndi mwamuna wina yemwe ndi ochilimika pa nkhani za ulimi. Banjalo linali lachitsanzo chifukwa choti anthu awiriwo amakonda kupemphera kusiyana ndi m’mene amakhalira ndi mwamuna oyambayo. Tsiku lina mwamuna wakeleyo anafika pa nkhomoko ndikuyamba kulalata ndipo mkanganowo utakula ndeu yoopsya inabuka mpaka mwini banjalo kukomoka . Anthu ena anatengera mkuluyo ku chipatala komwe sakupeza bwino, Nyakwawa ya m’mudzimo zadzudzula achinyamata awiriwo ndipo awayitanitsa kwa mfumu kuti akayankhe mlandu ndipo mfumuyo yaopsyeza kuti itengera nkhaniyi kwa akulu akulu achitetezo cha m’mudzimo

Get Your Newsletter