21/04/15

Written by  Newsroom

Mayi wina athawisana ndi ogulisa fodya
Anthu okhala ku Bilila m’boma la Ntcheu ati akudabwa ndi zomwe wachita mai wina posiya mwamuna wake yemwe anaberekerana naye ana asanu ndikuthawisana ndi mnyamata wina yemwe amakugula fodya mderalo.

27
April

Nkhaniyi ikuti maiyo amagwira ntchito yotungila madzi za njelwa pa bwana wina. Koma tsiku lina akuchokera ku mtsinje komwe anakatunga madzi anangoti gululu ndi njondayo. Mnyamatayo anagwa mchikondi ndi maiyo ngakhale maiyo anamufotokozera mnyamatayo ,kuti ali pa banja. Anthu awiriwo anagwa mchikondi mpaka tsiku lina maiyo anakagona ku malo komwe amagulira fodya-yo. Koma atazindikira kuti mwamuna wake waddziwa za nkhaniyi anthu awiliwo anagwirizana kuti asinthe malo ogulira fodyayo ndipo athawitsana kupita ku Bwanje m’boma lomwelo. Mnyamatayo wanenetsa kuti sansiya maiyo ngakhale ali ndi ana asanu chifukwa chaulemu omwe akulandila kwa iye. Pakadali pano mwamunayo wakatula nkhaniyi kwa nkhoswa komanso kwa akuluakulu ampingo kuti athandize chifukwa choti iye akuti sakwanitsa kulera anawo okha. Pakadali pano nyakwawa ya m’mudzimo yayitanitsa maiyo chifukwa choti anawo akusowa chisamaliro chokwanira.



Akomoka tsiku lonse atamwa tameki
Mkulu wina ku Golomoti m’boma la Ntcheu wapulumuka dzenje lokumbakumba atakomoka tsiku la thuthu atamwa tameki. Nkhaniyi ikuti mkazi wa bamboyo wakhala akudzudzula mkuluyo zakhalidwe lake lauchidakwa, Mkazi wa mkuluyo wakhala akuuza mwamunayo kuti asiye mkhalidwelo ati poganizira banjalo limagona mchisakasa chifukwa choti ndalama zomwe bamboyo akupeza zikuthera ku mowa. Mwamunayo atawona kuti mkazi wake akumusowetsa mtendere anaganiza zomwa tameki kuti adziphe , izi zinathekadi koma zinthu zinafika povuta pomwe mkuluyo anakomoka ati kambakoti anatsekula mmimba modetsa nkhawa. Anthu ena ataona kuti bamboyo wadwala kwambiri anathamangira naye kuchipatala komwe anatsimikiza kuti bamboyo anamwa tameki. Nyakwawa ya m’mudzimo yaopseza mkuluyo kuti alipa chindapusa ati kamba koti wanyazitsa mudziwo. Pakadali pano mwamunayo sakupeza bwino .

Get Your Newsletter