21/04/15

Written by  Newsroom

Mphongo ziwiri zikunthana mpaka kuchosana mano

Amuna awili anakunthana kodetsa nkhawa mpaka kuchotsana mano pamudzi wina kwa Che Somba mboma la Blantyre.

21
April

Chinatsitsa dzaye kuti njobvu ithyike nyanga malinga ndi amene watumiza nkhani-yi mkulu wina amagula mbadyila pamsika wina kumene-ko pamene anagwetsa memory card ya mufoni yake. Momwe amagwetsa kadiyo nkuti mkulu wina akumuuna ndipo anaiponda kudikilila kuti mwini wakeyo achokepo kaye. Komabe akuti anazindikila msanga kuti wataya kadi yake ndipo anadabwa ndi momwe mkulu yemwe anali pamalowo ananyamukila kumapita. Atamuyimitsa akuti amakana koma anthu ena analoza mkuluyo kuti chilipo chomwe anatola. Mosakhalitsa mwini kadi uja anambwandila nzakeyo ndikuyamba kumutikita mpaka anatulutsa memory kadi ija manu ake awili ali m’manja. Mwini memory anati sangachitile mwina polingalila kuti mu kadiyo muli nyimbo yomwe amaikonda ya Tchovetchove ya Oga Family. Panopa, mkulu wakuba uja akuti akadandaula kubwalo kuti nzake wamuchotsa mano apa mphumi.


Mai wina alowera mwamuna osapola mchombo
Mai wina kwa Mkwepu mdela la Makhetha mu mzinda wa Blantyre akuyenda mogwetsa nkhope yake pansi atamutulukila kuti wakalowelela m’nyamata wina osapola pamchombo. Nkhaniyi ikuti mwamuna wa mayiyo adapita ku Joni mdziko la South Africa komwe akugwila ntchito. Koma m’buyo muno mkazi wake anayamba kuzedmbelana ndi m’nyamata wina ogulitsa tchipisi mpaka chibwe nzi chao chinafumbila. Tsono mosakhalitsa m’nyamata uja ananyengelela mai uja kuti nthawi zina azikagona kunyumba kwake mpaka zinathekadi. Koma mphuno salota achibale ake amwamuna nkhani-yi inawapeza mpaka tsiku lina anamugwila okha akuchita zachisembwere ndi m’nyamatayo ndipo apa anadziwitsa mchimwene wao ku joni. Panopa, mwamuna wa mayiyo wamuuzilatu kuti aone msana wanjila azipita kwao ati kamba kolephela kuyamika pa zabwino zomwe amamuchitila. Pakadali pano, mayiyo akuti ngakhale mbale akumatsukila m’nyumba chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi atadziwa kuti yafala mdela lonselo.

Get Your Newsletter