20/04/15

Written by  Newsroom

Azindikira kuti akudyetsedwa konda ine

Mwamuna wina wakwa Zinganguwo ku Sigelege mu mzinda wa Blantyre akuyenda ali khuma khuma, kudandaula atatulukira kuti mkazi wake adamudyetsa kondaine.

21
April

Nkhani-yi ikuti mkazi woyamba wa bamboyo adamwalira atabeleka naye ana atatu ndipo anakwatira wina yemwe panopa ali ndi mapasa. Koma mkazi watsopanoyo akuti ndiwa uve ndiponso wa maganizo achibwana chifukwa chokonda za mankhwala achikuda. Masiku apitawa, mwamuna wake anagula matumba awiri a chimanga wolemera 5-kilograms lililonse koma mkaziyo anawaduduluza kupita nawo kwa sing’anga ncholinga choti ampatse kondaine kuti mwamuna wakeyo adzizungulira khonde. Panopa, mwamuna wake waima mutu ndi nkhaniyi komanso chifukwa choti ana pa nyumbapo akugona ndi njala kusowa chakudya ndipo maiyo akamufunsa za nkhaniyi akuyankha mokhadzula.



Mbuzi ibeleka mwana odabwisa
Mbuzi ya mkulu wina pamudzi wa Mwisa ku Mozambique yabeleka mwana odabwitsa kwambili. Malinga ndi amene watumiza nkhaniyi mkulu wina am’buzi yake inali ndi bere kuti iswe ana. Koma masiku ake atakwana obeleka mwini chifuyocho anadabwa kuona kuti mbuziyo yabelela chinthu chomwe chimaonetsa kuti mbali inayi mbuzi koma mutuwu chinyama chosadziwika. Pa chifukwa ichi, akuti anayamba kumemeza anthu kuti adzaone zamalodzazo. Chinthucho akuti sichidakhalitse chinafa ndipo anthu amene aona zimene ati chinthucho chinali ndi diso limodzi pamphumi komanso miyendo yoposa inayi. Panopa, chinthu-cho achikwilila ndipo mwini chifuyo-cho akuti akukonza zongogulitsa manthu yemwe anabeleka zamalodzazo.

Get Your Newsletter