19/04/15

Written by  Newsroom

Chipwilikiti pa maliro 

Kunali chipwilikiti pa maliro ena omwe anachitika m’mudzi wina kwa T/A Chadza mboma la Lilongwe pamene adzukulu anasemphana maganizo ndi Mfumu ya m’mudzimo.

21
April

Nkhaniyi ndi yakuti amai ambiri m’mudzimo ali ndi mchitidwe oyipa otchova juga amuna ao akachoka pakhomo. Poona kuti khalidweli lakhala likupasula mabanja ambiri m’mudzimo a Mfumu anadzudzula khalidwelo ndikulamula kuti aliyense yemwe apezeke akuchita izi adzamulipilitsa nkhuku. Koma atalankhula izi pa malilopo adzukulu anadzuma ndikutsutsana ndi maganizowo ponena kuti chilangocho chachepa koma m’malo mwake anthuwo adzilipitsidwa mbuzi yathunthu. Adzukuluwo anachita izi ati chifukwa choti iwonso akukhudzidwa kwambiri ndi khalidwe lonyansalo chifukwa choti ambiri mwa amayiwo ndi akazi awo. Koma izi sizinasangalatse Mfumuyo malinga nkuti ati zinaoneka ngati adzukuluwo akuderela posemphana ndi chigamulo chake mpaka kunakhala kusamvetsetsana pa malo asiwao. Pakadali pano mfumuyo yaopyseza kuti iyitanila ku bwalo adzukuluwo ati chifukwa chomuderela. Koma nawonso adzukuluwo amenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti sakaponda bwalolo chifukwa ati Mfumuyo imalekerela zinthu zolakwika zambiri zomwe zimachitika m’mudzimo.

 

Akunthidwa kamba kophunzitsa ana ufiti
Chipwilikiti china buka m’mudzi wa Ng’ong’ola kwa Mkanda mboma la Mulanje pamene makolo a ana omwe ati akuwaganizila kuti amaphunzitsidwa ufiti atamenya kolapitsa anthu omwe amawaganizila kuti amaphunzitsa anao ufiti. Nkhani yonse ikuti ana ena achichepere mudzimo anagwirizana zokaulula kwa makolo awo kuti anthu ena akuwaphunzitsa ufiti ndipo anawaveka nyota zoti aphe makolo awo m’matsenga. Makolo a anawo atamva izi anagwirizana zothana ndi anthu omwe anawatchulawo ndipo anakawathidzimula kolapitsa mpaka enewo kuwavulaza. Mfumu ya mudziwo itamva izi, inaitanitsa anthuwo ndikuwauza kuti zomwe achita sizabwino ponena kuti zomwe anena anawo zinalibe umboni. Mfumuyo inalamula anthuwo kulipila chindapusa cha 2-thousand kwacha aliyense kuti zina mwa ndalamazo apite ndi anthuwo kuchipatala. Malipoti ati anthu ena mudzimo ndiwosakondwa ndi chigamulocho ati chifukwa choti mudzimo mumachitika nkhani zaufiti zambiri komanso ati ana nthawi zambiri samanama.

Get Your Newsletter