Khaniyi ikuti mayiyo anapita kwa Singangayo kuti amuthandize mankhwala oti achoke m’matsoka omwe amakomana nawo, koma Sing’angayo sanavute ndipo anatsimikizila mayiyo kuti imeneyo si nkhani ndipo afika kumalo oyenerela. Sing’angayo anauza mayiyo kuti akabwere mawa lake pamodzi ndi mamuna wake. Atafika anauza payiyo kuti alowe koyambirila, apa anamuuza kuti avule zovala zonse ndikumuopyseza kuti akakuwa aona zakuda. Kumapeto kwake anauza bamboyo kuti alowe mkutseka ndi makiyi, koma chodabwitsa anauza bamboyo kuti vuto lomwe mkaziyo ali nayo kuti lithe mpofunika kuti agonane koma Sing’angayo akuonerela.
Anthu afa ndi phwete wakuba zitamuonekela
Anthu ochita malonda pa msika wa njala kwa Njovu mboma la Nsanje anafa ndi mphwete pa zomwe zinamuchitikira tsinzinamtole wina pa msikapo. Nkhani yonse ikuti Mnyamata wina wakhala akuzunza anthu pakuwabera pa msikapo komanso malo ena ozungulira malowo. Anthu apamalopo anagwirizana pulani yofuna kuthana ndi mkuluyo kuti mwina nkusiya khalidwe lake lakubalo. Iwo anauza munthu wina wa bizinesi wa mdera lina kuti aonetse kuti akugula zinthu ndikusiya powonekera bwino ku thumba lakumbuyo chikwama cha ndalama chofufuma bwino komano nkuyandikira dala mnyamatayo. Mnyamatayo anangoti laponda la mphawi ndipo anasolola chikwama cha mkuluyo koma chodabwitsa mchakuti mkuluyo sanatekeseke ndikuti amubera. Chodabwitsa anthu ena omwe anali pa msikawo mchakuti patadutsa nthawi yochepa mbalayo inabwerela uku ikulira nkunena kuti chonde mundikhululukire ndasiya kuba. Mpompanikiza kuti anthu ena amutengere ku bwalo la Mfumu analapa ndikunena kuti waona zakuda atapeza masamba apapaya mchikwamacho koma pakati pa masambawo panali mau onena kuti SIYANI KUBA MUDZAONA ZAKUDA KOMA KWALERO TAKUKHULULUKIRANI. Apa anthuwo anagwirizana zomukhululukira ndikumulangiza kuti asiye khalidwe lake lakuba, koma munthu yemwe anamuberayo sanaonekenso.