Mkulu wina afufuma nkhope ngati chitumbuwa
Mkulu wina wapa mudzi wa Bazirio m’boma la Mchinji akubindikira m’nyumba kamba ka manyazi nkhope yake itafufuma monga chitumbuwa.
Mnyamata wina aba kabudula wachikazi musitolo
M’nyamata wina wa kabaza wapa mudzi wa Chipakuza ku Nchalo m’boma la Chikwawa watha masiku angapo asakupita ku geni yake mbiri itawanda kuti anamugwira akuba kabudula wa mkati m’sitolo ina yotchuka kumeneko.
Dalaivala ayenda zamadulira atagulisa engine
Dalaivala wina ku Chilomoni mu mzinda wa Blantyre akuti wathawa ndipo akungoyendayenda mtchire powopa achitetezo omwe akumufunafuna pomuganizira kuti agulitsa engine ya galimoto yomwe amayendera.
Gogo wina auka kwa akufa
Anthu akwa Gunda mdera la Jenala ku Phalombe akukhala mwa mantha chifukwa cha zomwe zawachitikira.