Asekedwa kamba ka nkhuli
Mwamuna wina akumuseka kwa Sub-T.A. Ngwelero m’boma la Zomba kamba ka nkhuli yomwe ali nao.
M'busa agwidwa akusamba usiku panja
Mbusa wampingo wina kwa Mgona A ku Kanengo mu mzinda wa Lilongwe akuyenda mogwetsa nkhope yake pansi chifukwa cha manyazi atamutulukila kuti amasamba usiku uli onse 10 –kokolo kwinaku akuzungulila nyumba.
Kuponi iwutsa mapiri pa chigwa
Kuponi yolandilira mbeu ndi feteleza zotsika mtengo yautsa mapiri pa chigwa pa mudzi wa Makuta kwa Kalembo m’boma la Balaka. Nkhaniyi ikuti masiku apitawa kunabuka mkangano ku banja lina pa mudzipo.
Mkulu wina alipira chi ndapusa atamenya mkazi wake pa maliro
Chidakwa china chapa mudzi wa Njuzi kwa Likoswe m’boma la Chiradzulu achilamula kuti chilipire mbuzi imodzi ndi nkhuku zitatu ku bwalo la anyakwawa kamba kokuntha mkazi wake pa maliro.