Athawa kunyumba ataba foni yam'manja
Mtsikana wina ku Chilomoni mu mzinda wa Blantyre wathawa kwao ataba foni ya m’manja ya m’bale wake ndipo akungotandala powopa kumulanda foniyo komanso kumuswa.
Amuophyeza kuti amukanyanga popanda chifukwa
Venda wina yemwe ntchito yake ndi yobulasha nsapato za anthu kuseli kwa malo okwelera minibus zopita ku Nkolokosa mu mzinda wa Blantyre akudandaula chifukwa cha venda mzake wogulitsa malamba yemwe walumbira kuti amuphwasula ati popanda chifukwa.
Achilapa atagulisa malo kwa anthu awiri
Bambo wina kwa Wimbe m’boma la Kasungu wanenetsa kuti wasiya khalidwe lake lautambwali atagulitsa munda wake kwa anthu awiri mzaka zosiyana.
Okonda kuzembelera akazi aeni alandidwa ndalama
Mkulu wina wakwa Chikowi m’boma la Zomba wotchuka ndikuzembera akazi a weni awona polekera atalandidwa ndalama zake zonse za malipilo ndi njinga yakapalase yomwe imamuthandizila kupita ku ntchito.