Abetsa katundu kamba ka nsanje
Mai wina kwa Chamthunya mboma la Balaka akuyenda ali zoli zoli ngati wataya singano atabetsa katundu wam’nyumba chifukwa cha sanje.
Mafumu awiri afuna kukunthana
Mafumu awili omwenso ndipa chibale anafuna kufafanthana pamwambo olambula kumanda pamudzi wina kwa Phambala mboma la Ntcheu.
Alandidwa katundu yense wa mnyumba
Anthu a kwa Mfumu Mnyanja m’boma la Kasungu anafa ndi chikhakhali mkulu wina yemwe amatsogolera kulanda anthu zinthu nayenso analandidwa katundu yense wa mnyumba.
Athetsa banja kamba ka nsanje
Mfumu yina kwa Nsamala m’boma la Balaka yathetsa banja lake chifukwa cha msanje.